Pakuti, onani, oipa akoka uta, apiringidza muvi wao pansinga, kuwaponyera mumdima oongoka mtima.
Masalimo 64:3 - Buku Lopatulika Amene anola lilime lao ngati lupanga, napiringidza mivi yao, ndiyo mau akuwawitsa; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Amene anola lilime lao ngati lupanga, napiringidza mivi yao, ndiyo mau akuwawitsa; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iwo amanola lilime lao ngati lupanga, amaponya mau obaya ngati mivi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo amanola malilime awo ngati malupanga, amaponya mawu awo olasa ngati mivi. |
Pakuti, onani, oipa akoka uta, apiringidza muvi wao pansinga, kuwaponyera mumdima oongoka mtima.
Mundisunge ndisagwe mumsampha ananditcherawo, ndisakodwe m'makwekwe a iwo ochita zopanda pake.
Moyo wanga uli pakati pa mikango; ndigona pakati pa oyaka moto, ndiwo ana a anthu amene mano ao ali nthungo ndi mivi, ndipo lilime lao ndilo lupanga lakuthwa.
Pali mbadwo mano ao akunga malupanga, zibwano zao zikunga mipeni; kuti adye osauka kuwachotsa kudziko, ndi aumphawi kuwachotsa mwa anthu.
Palibe chida chosulidwira iwe chidzapindula; ndipo lilime lonse limene lidzakangana nawe m'chiweruzo udzalitsutsa. Ichi ndi cholowa cha atumiki a Yehova, ndi chilungamo chao chimene chifuma kwa Ine, ati Yehova.
Ndipo apinda lilime lao ngati uta wao, liname; koma akula mphamvu m'dzikomo, koma si pachoonadi; pakuti alinkunkabe nachita zoipa, ndipo sandidziwa Ine, ati Yehova.