Mukumbukire Yehova kuti ndinayendabe pamaso panu m'choonadi, ndi mtima wangwiro, ndi kuchita zokoma m'kuona kwanu. Nalira Hezekiya kulira kwakukulu.
Masalimo 6:7 - Buku Lopatulika Lapuwala diso langa chifukwa cha chisoni; lakalamba chifukwa cha onse akundisautsa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Lapuwala diso langa chifukwa cha chisoni; lakalamba chifukwa cha onse akundisautsa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Maso anga atupa chifukwa cha kulira, afooka chifukwa cha adani anga onse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Maso anga atupa chifukwa cha chisoni; akulephera kuona chifukwa cha adani anga. |
Mukumbukire Yehova kuti ndinayendabe pamaso panu m'choonadi, ndi mtima wangwiro, ndi kuchita zokoma m'kuona kwanu. Nalira Hezekiya kulira kwakukulu.
M'diso mwanga muchita chizirezire chifukwa cha chisoni, ndi ziwalo zanga zonse zilibe chithunzi.
Mtima wanga ugundagunda, mphamvu yanga yachoka, ndipo kuunika kwa maso anga, ndi iko komwe kwandichokera.
Ondida kopanda chifukwa achuluka koposa tsitsi la pamutu panga; ofuna kunditha, ndiwo adani anga monama, ali ndi mphamvu. Pamenepo andibwezetsa chosafunkha ine.
Diso langa lapuwala chifukwa cha kuzunzika kwanga: Ndimaitana Inu, Yehova, tsiku lonse; nditambalitsira manja anga kwa Inu.
Munati, Kalanga ine tsopano! Pakuti Yehova waonjezera chisoni pa zowawa zanga; ndalema ndi kubuula kwanga, sindipeza kupuma.