Maneno anga awulula chiongoko cha mtima wanga, ndi monga umo idziwira milomo yanga idzanena zoona.
Masalimo 49:3 - Buku Lopatulika Pakamwa panga padzanena zanzeru; ndipo chilingiriro cha mtima wanga chidzakhala cha chidziwitso. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakamwa panga padzanena zanzeru; ndipo chilingiriro cha mtima wanga chidzakhala cha chidziwitso. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zosinkhasinkha za mtima wanga zidzakhala zakuya, ndipo ndidzalankhula zanzeru. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakamwa panga padzayankhula mawu anzeru; mawu ochokera mu mtima mwanga adzapereka nzeru. |
Maneno anga awulula chiongoko cha mtima wanga, ndi monga umo idziwira milomo yanga idzanena zoona.
Mau a m'kamwa mwanga ndi maganizo a m'mtima wanga avomerezeke pamaso panu, Yehova, thanthwe langa, ndi Mombolo wanga.
Koma dziwani kuti Yehova anadzipatulira yekha womkondayo, adzamva Yehova m'mene ndimfuulira Iye.
Mtima wanga usefukira nacho chinthu chokoma. Ndinena zopeka ine za mfumu, lilime langa ndilo peni yofulumiza kulemba.
Munthu wabwino atulutsa zabwino m'chuma chake chabwino, ndi munthu woipa atulutsa zoipa m'chuma chake choipa.
Chiphunzitso changa chikhale ngati mvula; maneno anga agwe ngati mame; ngati mvula yowaza pamsipu, ndi monga madontho a mvula pazitsamba.