Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Mateyu 12:35 - Buku Lopatulika

35 Munthu wabwino atulutsa zabwino m'chuma chake chabwino, ndi munthu woipa atulutsa zoipa m'chuma chake choipa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

35 Munthu wabwino atulutsa zabwino m'chuma chake chabwino, ndi munthu woipa atulutsa zoipa m'chuma chake choipa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

35 Munthu wabwino amatulutsa zabwino m'chuma chabwino cha mumtima mwake. Nayenso munthu woipa amatulutsa zoipa m'chuma choipa cha mumtima mwake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

35 Munthu wabwino amatulutsa zinthu zabwino zomwe zili mumtima mwake ndipo munthu woyipa amatulutsanso zinthu zoyipa zomwe zili mwa iye.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 12:35
17 Mawu Ofanana  

amene aja sangakuphunzitse, ndi kukufotokozera, ndi kutulutsa mau a mumtima mwao?


Mau a oipa abisalira mwazi; koma m'kamwa mwa olungama muwalanditsa.


Munthu akondwera ndi mayankhidwe a m'kamwa mwake; ndi mau a pa nthawi yake kodi sali abwino?


Mtima wa wolungama uganizira za mayankhidwe; koma m'kamwa mwa ochimwa mutsanulira zoipa.


Kuchiza lilime ndiko mtengo wa moyo; koma likakhota liswa moyo.


Akubadwa inu a njoka, mungathe bwanji kulankhula zabwino, inu akukhala oipa? Pakuti m'kamwa mungolankhula mwa kusefuka kwake kwa mtima.


Ndipo Iye anati kwa iwo, Chifukwa chake, mlembi aliyense, wophunzitsidwa mu Ufumu wa Kumwamba, ali wofanana ndi munthu mwini banja, amene atulutsa m'chuma chake zinthu zakale ndi zatsopano.


Chomwecho mtengo wabwino uliwonse upatsa zipatso zokoma; koma mtengo wamphuchi upatsa zipatso zoipa.


Munthu wabwino atulutsa zabwino m'chuma chokoma cha mtima wake; ndi munthu woipa atulutsa zoipa m'choipa chake: pakuti m'kamwa mwake mungolankhula mwa kuchuluka kwa mtima wake.


Nkhani yonse yovunda isatuluke m'kamwa mwanu, koma ngati pali ina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo, kuti ipatse chisomo kwa iwo akumva.


Mau a Khristu akhalitse mwa inu chichulukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalimo, ndi mayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuimbira Mulungu ndi chisomo mumtima mwanu.


Mau anu akhale m'chisomo, okoleretsa, kuti mukadziwe inu mayankhidwe anu a kwa yense akatani.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa