Ndipo ndinawerama mutu wanga ndi kulambira Yehova, ndi kumyamikira Yehova, Mulungu wa mbuyanga Abrahamu, amene ananditsogolera ine m'njira yakuona, kuti ndikamtengere mwana wamwamuna wake mwana wa mkazi wa mphwake wa mbuyanga.
Masalimo 32:8 - Buku Lopatulika Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo; ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang'ana iwe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo; ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang'ana iwe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta akuti, “Ndidzakudziŵitsa ndi kukuphunzitsa njira imene uyenera kuyendamo. Ndidzakulangiza ndi kukuyang'anira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndidzakulangiza ndi kukuphunzitsa njira imene udzayendamo; ndidzakupatsa uphungu ndi kukuyangʼanira. |
Ndipo ndinawerama mutu wanga ndi kulambira Yehova, ndi kumyamikira Yehova, Mulungu wa mbuyanga Abrahamu, amene ananditsogolera ine m'njira yakuona, kuti ndikamtengere mwana wamwamuna wake mwana wa mkazi wa mphwake wa mbuyanga.
pamenepo mverani Inu mu Mwamba, ndi kukhululukira tchimo la akapolo anu, ndi la anthu anu Aisraele; pakuti muwaphunzitsa njira yokoma ayenera kuyendamo, ndi kupatsa mvula padziko lanu, limene munawapatsa anthu anu likhale cholowa chao.
Mundimvetse chifundo chanu mamawa; popeza ndikhulupirira Inu: Mundidziwitse njira ndiyendemo; popeza ndikweza moyo wanga kwa Inu.
Atero Yehova, Mombolo wako, Woyera wa Israele, Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m'njira yoyenera iwe kupitamo.
Iwo sadzakhala ndi njala, pena ludzu; ngakhale thukuta, pena dzuwa silidzawatentha; pakuti Iye amene wawachitira chifundo, adzawatsogolera, ngakhale pa akasupe a madzi adzawatsogolera.
Ngakhale masiku awiri, kapena mwezi, kapena masiku ambiri, pokhalitsa mtambo pamwamba pa chihema ndi kukhalapo, ana a Israele anakhala m'chigono, osayenda ulendo; koma pakukwera uwu, anayenda ulendo.
Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.