nati iye, Tamverani Ayuda inu nonse, ndi inu okhala mu Yerusalemu, ndi inu mfumu Yehosafati, atero nanu Yehova, Musaope musatenge nkhawa chifukwa cha aunyinji ambiri awa; pakuti nkhondoyi si yanu, koma ya Mulungu.
Masalimo 27:3 - Buku Lopatulika Lingakhale gulu la ankhondo limanga misasa kuti andithyole, mtima wanga sungachite mantha; ingakhale nkhondo ikandiukira, inde pomweponso ndidzakhulupirira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Lingakhale gulu la ankhondo limanga misasa kuti andithyole, mtima wanga sungachite mantha; ingakhale nkhondo ikandiukira, inde pomweponso ndidzakhulupirira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ngakhale gulu lankhondo lindizinge, mtima wanga sudzachita mantha konse. Ngakhale nkhondo ibuke kulimbana nane, ine sindidzaleka kukhulupirira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngakhale gulu lankhondo lindizinge, mtima wanga sudzaopa. Ngakhale nkhondo itayambika kulimbana nane, ngakhale nthawi imeneyo, ine ndidzalimbika mtima. |
nati iye, Tamverani Ayuda inu nonse, ndi inu okhala mu Yerusalemu, ndi inu mfumu Yehosafati, atero nanu Yehova, Musaope musatenge nkhawa chifukwa cha aunyinji ambiri awa; pakuti nkhondoyi si yanu, koma ya Mulungu.
Kodi kulimbika mtima kwako si ndiko kuti uopa Mulungu, ndi chiyembekezo chako si ndiwo ungwiro wa njira zako?
Ukani Yehova; ndipulumutseni, Mulungu wanga! Pakuti mwapanda adani anga onse patsaya; mwawathyola mano oipawo.
osaopa adani m'kanthu konse, chimene chili kwa iwowa chisonyezo cha chionongeko, koma kwa inu cha chipulumutso, ndicho cha kwa Mulungu;
Komatu ngatinso mukumva zowawa chifukwa cha chilungamo, odala inu; ndipo musaope pakuwaopa iwo, kapena musadere nkhawa;
Usaope zimene uti udzamve kuwawa; taona, mdierekezi adzaponya ena a inu m'nyumba yandende, kuti mukayesedwe; ndipo mudzakhala nacho chisautso masiku khumi. Khala wokhulupirika kufikira imfa, ndipo ndidzakupatsa iwe korona wa moyo.
Ndipo kunalinso nkhondo; ndipo Davide anatuluka, nakamenyana ndi Afilisti, nawapha ndi maphedwe aakulu, ndipo iwo anamthawa iye.