Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Afilipi 1:28 - Buku Lopatulika

28 osaopa adani m'kanthu konse, chimene chili kwa iwowa chisonyezo cha chionongeko, koma kwa inu cha chipulumutso, ndicho cha kwa Mulungu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

28 osaopa adani m'kanthu konse, chimene chili kwa iwowa chisonyezo cha chionongeko, koma kwa inu cha chipulumutso, ndicho cha kwa Mulungu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

28 osalola kuti adani anu azikuwopsezani pa kanthu kalikonse. Zimenezi zidzaŵatsimikizira kuti iwowo adzaonongeka, koma inu mudzapulumuka. Mulungu ndiye amene adzakuchitirani zimenezi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

28 osachita mantha ndi pangʼono pomwe ndi amene akutsutsana nanu. Ichi ndi chizindikiro kwa iwo kuti adzawonongedwa, koma inu mudzapulumutsidwa ndi Mulungu.

Onani mutuwo Koperani




Afilipi 1:28
24 Mawu Ofanana  

Ndadikira chipulumutso chanu, Yehova.


Wopereka nsembe yachiyamiko andilemekeza Ine; ndipo kwa iye wosunga mayendedwe ake ndidzamuonetsa chipulumutso cha Mulungu.


Taonani, Mulungu ndiye chipulumutso changa; ndidzakhulupirira, sindidzaopa; pakuti Yehova Mwini ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, Iye ndiye chipulumutso changa.


Ine, Inedi, ndine amene nditonthoza mtima wako; kodi iwe ndani, kuti uopa munthu amene adzafa, ndi mwana wa munthu amene adzakhala ngati udzu;


Mverani Ine, inu amene mudziwa chilungamo, anthu amene mumtima mwao muli lamulo langa; musaope chitonzo cha anthu, ngakhale kuopsedwa ndi kutukwana kwao.


Ndipo musamaopa amene akupha thupi, koma moyo sangathe kuupha; koma makamaka muope Iye, wokhoza kuononga moyo ndi thupi lomwe muGehena.


Ndipo ananena ndi munthu ali ndi dzanja lopuwala, Taimirira pakati.


ndipo anthu onse adzaona chipulumutso cha Mulungu.


Ndipo atadza Iyeyo, adzatsutsa dziko lapansi za machimo, ndi za chilungamo, ndi za chiweruziro;


Potero, dziwani inu, kuti chipulumutso ichi cha Mulungu chitumidwa kwa amitundu; iwonso adzamva.


ndipo ngati ana, pomweponso olowa nyumba; inde olowa nyumba ake a Mulungu, ndi olowa anzake a Khristu; ngatitu ife timva zowawa pamodzi naye, kuti tikalandirenso ulemerero pamodzi ndi Iye.


koma tingakhale tidamva zowawa kale, ndipo anatichitira chipongwe, monga mudziwa, ku Filipi, tinalimbika pakamwa mwa Mulungu wathu kulankhula ndi inu Uthenga Wabwino wa Mulungu m'kutsutsana kwambiri.


Kotero kuti tinena molimbika mtima, Mthandizi wanga ndiye Ambuye; sindidzaopa; adzandichitira chiyani munthu?


Usaope zimene uti udzamve kuwawa; taona, mdierekezi adzaponya ena a inu m'nyumba yandende, kuti mukayesedwe; ndipo mudzakhala nacho chisautso masiku khumi. Khala wokhulupirika kufikira imfa, ndipo ndidzakupatsa iwe korona wa moyo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa