Ndipo Davide anadzimangira nyumba m'mzinda mwake, nakonzeratu malo likasa la Mulungu, naliutsira hema.
Masalimo 24:3 - Buku Lopatulika Adzakwera ndani m'phiri la Yehova? Nadzaima m'malo ake oyera ndani? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Adzakwera ndani m'phiri la Yehova? Nadzaima m'malo ake oyera ndani? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndani angayenere kukwera phiri la Chauta? Ndani angaime m'malo ake oyera? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndani angakwere phiri la Yehova? Ndani angathe kuyima pa malo ake opatulika? |
Ndipo Davide anadzimangira nyumba m'mzinda mwake, nakonzeratu malo likasa la Mulungu, naliutsira hema.
Wodala munthuyo mumsankha, ndi kumyandikizitsa, akhale m'mabwalo anu. Tidzakhuta nazo zokoma za m'nyumba yanu, za m'malo oyera a Kachisi wanu.
Munakwera kunka kumwamba, munapita nao undende kuuyesa ndende; munalandira zaufulu mwa anthu, ngakhale mwa opikisana nanu, kuti Yehova Mulungu akakhale nao.
Ndipo Yehova anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, samalira bwino, nupenye ndi maso ako, numve m'makutu mwako zonse ndidzanena nawe, kunena za malemba onse a nyumba ya Yehova, ndi malamulo ake onse; nusamalire bwino malowedwe a nyumbayi, ndi matulukidwe ake onse a malo opatulika.
Atero Ambuye Yehova, Palibe mlendo wosadulidwa m'mtima, wosadulidwa m'thupi, alowe m'malo anga opatulika, mwa alendo onse ali pakati pa ana a Israele.
Ndipo Mose anati kwa Aroni, Ichi ndi chimene Yehova ananena, ndi kuti, Mwa iwo akundiyandikiza ndipatulidwa Ine, ndi pamaso pa anthu onse ndilemekezedwa. Ndipo Aroni anakhala chete.
Taonani, ndituma mthenga wanga, kuti akonzeretu njira pamaso panga; ndipo Ambuye amene mumfuna adzadza ku Kachisi wake modzidzimutsa; ndiye mthenga wa chipangano amene mukondwera naye; taonani akudza, ati Yehova wa makamu.
Simoni Petro anena ndi Iye, Ambuye, mumuka kuti? Yesu anayankha, Kumene ndimukako sungathe kunditsata Ine tsopano; koma, udzanditsata bwino lomwe.
Yesu ananena naye, Usandikhudze, pakuti sinditha kukwera kwa Atate; koma pita kwa abale anga, ukati kwa iwo, Ndikwera kunka kwa Atate wanga, ndi Mulungu wanu.
Mwa ichi polandira ufumu wosagwedezeka, tikhale nacho chisomo, chimene tikatumikire nacho Mulungu momkondweretsa, ndi kumchitira ulemu ndi mantha.