Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mbiri 15:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo Davide anadzimangira nyumba m'mzinda mwake, nakonzeratu malo likasa la Mulungu, naliutsira hema.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo Davide anadzimangira nyumba m'mudzi mwake, nakonzeratu malo likasa la Mulungu, naliutsira hema.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Davide adadzimangira nyumba zina mu mzinda wa Davide. Adakonza malo a Bokosi lachipangano la Chauta, namanga hema loikamo Bokosilo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Davide atadzimangira nyumba zina mu Mzinda wa Davide, iye anakonza malo a Bokosi la Mulungu ndipo analimangira tenti.

Onani mutuwo Koperani




1 Mbiri 15:1
14 Mawu Ofanana  

Ndipo mfumu inati, Apatukire kunyumba ya iye yekha, koma asaone nkhope yanga. Chomwecho Abisalomu anapatukira kunyumba ya iye yekha, wosaona nkhope ya mfumu.


Ndipo Davide anakhala m'linga muja, nalitcha mzinda wa Davide. Davide namanga linga pozinga ponse kuyambira ku Milo ndi m'kati momwe.


Pamenepo anthu anauza mfumu Davide, kuti Yehova wadalitsa banja la Obededomu ndi zake zonse, chifukwa cha likasa la Mulungu. Chomwecho Davide anamuka nakatenga likasa la Mulungu kunyumba ya Obededomu, nakwera nalo kumzinda wa Davide, ali ndi chimwemwe.


Ndipo pamene adalowa nalo likasa la Mulungu analiika pamalo pake pakati pa hema amene Davide adaliutsira; ndipo Davide anapereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zoyamika pamaso pa Yehova.


Inu ndinu akulu a nyumba za makolo a Alevi, mudzipatule inu ndi abale anu omwe, kuti mukatenge ndi kukwera nalo likasa la Yehova Mulungu wa Israele ku malo ndalikonzera.


Ndipo Davide anasonkhanitsira Aisraele onse ku Yerusalemu, akwere nalo likasa la Yehova kumalo kwake adalikonzera.


Ndipo analowa nalo likasa la Mulungu, naliika pakati pa hemalo Davide adaliutsira; ndipo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika pamaso pa Mulungu.


Ndipo iwo aja Davide anawaimika a udindo wa nyimbo m'nyumba ya Yehova, litafikira kupumula likasalo, ndi awa.


Koma likasa la Mulungu Davide adakwera nalo kuchokera ku Kiriyati-Yearimu kunka kumene Davide adalikonzeratu malo; pakuti adaliutsiratu hema ku Yerusalemu.


Pamenepo Solomoni anasonkhanitsira akuluakulu a Israele, ndi akulu onse a mafuko, ndi akalonga a nyumba za makolo a ana a Israele, ku Yerusalemu, kukatenga likasa la chipangano cha Yehova kumzinda wa Davide ndiwo Ziyoni.


kufikira nditapezera Yehova malo, chokhalamo Wamphamvuyo wa Yakobo?


amene anapeza chisomo pamaso pa Mulungu, napempha kuti apeze mokhalamo Mulungu wa Yakobo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa