Ndine ngati munthu wosekedwa ndi mnansi wake, ndinaitana kwa Mulungu, ndipo anandiyankha; munthu wolungama wangwiro asekedwa.
Masalimo 22:7 - Buku Lopatulika Onse akundipenya andiseka; akwenzula, apukusa mutu, nati, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Onse akundipenya andiseka; akwenzula, apukusa mutu, nati, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Onse ondiwona amandiseka, amandikwenzulira ndi kupukusa mitu yao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Onse amene amandiona amandiseka; amandiyankhulira mawu achipongwe akupukusa mitu yawo kunena kuti |
Ndine ngati munthu wosekedwa ndi mnansi wake, ndinaitana kwa Mulungu, ndipo anandiyankha; munthu wolungama wangwiro asekedwa.
Iwo anandiyasamira pakamwa pao; anandiomba pama ndi kunditonza; asonkhana pamodzi kunditsutsa.
Inenso ndikadanena monga inu, moyo wanu ukadakhala m'malo mwa moyo wanga, ndikadalumikizanitsa mau akutsutsana nanu, ndi kukupukusirani mutu wanga.
Ikhale yosalankhula milomo ya mabodza, imene imalankhula mwachipongwe pa olungama mtima, ndi kudzikuza ndi kunyoza.
Atero Yehova, Mombolo wa Israele, ndi Woyera wake, kwa Iye amene anthu amnyoza, kwa Iye amene mtundu wathu unyasidwa naye, kwa mtumiki wa olamulira: Mafumu adzaona, nadzauka; akalonga nadzalambira chifukwa cha Yehova, amene ali wokhulupirika, ngakhale Woyera wa Israele, amene anakusankha Iwe.
Iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu; munthu wazisoni, ndi wodziwa zowawa; ndipo ananyozedwa monga munthu wombisira anthu nkhope zao; ndipo ife sitinamlemekeze.
Ndiye yani mudzikondweretsa momseka? Ndani mulikumyasamira kukamwa, ndi kumtulutsira lilime? Kodi inu simuli ana akulakwa, mbeu yonama?
Ndipo analuka korona waminga, namveka pamutu pake, namgwiritsa bango m'dzanja lamanja lake; ndipo anagwada pansi pamaso pake, namchitira chipongwe, nati, Tikuoneni, mfumu ya Ayuda!
ananena, Tulukani, pakuti kabuthuko sikanafe koma kali m'tulo. Ndipo anamseka Iye pwepwete.
Ndipo atatha kumnyoza anamvula chibakuwacho namveka Iye zovala zake. Ndipo anatuluka naye kuti akampachike Iye pamtanda.
Ndipo iwo akupitirirapo anamchitira mwano, napukusa mitu yao, nanena, Ha! Iwe wakupasula Kachisi, ndi kummanga masiku atatu,
Ndipo Herode ndi asilikali ake anampeputsa Iye, namnyoza, namveka Iye chofunda chonyezimira, nambwezera kwa Pilato.