Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 9:24 - Buku Lopatulika

24 ananena, Tulukani, pakuti kabuthuko sikanafe koma kali m'tulo. Ndipo anamseka Iye pwepwete.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 ananena, Tulukani, pakuti kabuthuko sikanafa koma kali m'tulo. Ndipo anamseka Iye pwepwete.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Tsono Iye adaŵauza kuti, “Tatulukani! Mtsikanayutu sadamwalire ai, ali m'tulo chabe.” Pamenepo anthuwo adayamba kumseka monyodola.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 anati, “Tulukani, mtsikanayu sanafe koma ali mtulo.” Koma anamuseka Iye.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 9:24
12 Mawu Ofanana  

Ndine ngati munthu wosekedwa ndi mnansi wake, ndinaitana kwa Mulungu, ndipo anandiyankha; munthu wolungama wangwiro asekedwa.


Atero Yehova, Mombolo wa Israele, ndi Woyera wake, kwa Iye amene anthu amnyoza, kwa Iye amene mtundu wathu unyasidwa naye, kwa mtumiki wa olamulira: Mafumu adzaona, nadzauka; akalonga nadzalambira chifukwa cha Yehova, amene ali wokhulupirika, ngakhale Woyera wa Israele, amene anakusankha Iwe.


Iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu; munthu wazisoni, ndi wodziwa zowawa; ndipo ananyozedwa monga munthu wombisira anthu nkhope zao; ndipo ife sitinamlemekeze.


Ndipo anamseka Iye pwepwete. Koma Iye anawatulutsa onse, natenga atate wa mwana, ndi amake, ndi ajawo anali naye, nalowa m'mene munali mwanayo.


Ndipo anamseka Iye pwepwete podziwa kuti anafa.


Koma Yesu pamene anamva, anati, Kudwala kumene sikuli kwa imfa, koma chifukwa cha ulemerero wa Mulungu, kuti Mwana wa Mulungu alemekezedwe nako.


Ndipo potsikirako Paulo, anamgwera namfungatira, nati, Musachite phokoso, pakuti moyo wake ulipo.


Koma Petro anawatulutsa onse, nagwada pansi, napemphera; ndipo potembenukira kumtembo anati, Tabita, uka. Ndipo anatsegula maso ake; ndipo pakuona Petro, anakhala tsonga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa