Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 9:23 - Buku Lopatulika

23 Ndipo Yesu polowa m'nyumba yake ya mkuluyo, ndi poona oimba zitoliro ndi khamu la anthu obuma,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Ndipo Yesu polowa m'nyumba yake ya mkuluyo, ndi poona oimba zitoliro ndi khamu la anthu obuma,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Pamene Yesu adafika kunyumba kwa mkulu uja, adaona anthu oimba zitoliro, ndiponso anthu ambiri obuma.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Yesu atalowa mʼnyumba ya mkulu wa sunagoge ndi kuona oyimba zitoliro ndi gulu la anthu ochita phokoso,

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 9:23
12 Mawu Ofanana  

Ndipo Yeremiya anamlembera Yosiya nyimbo yomlira; ndi oimbira onse, amuna ndi akazi, amanena za Yosiya nyimbo za maliro zao mpaka lero lino; naziika zikhale lemba mu Israele; taonani, zilembedwa mu Nyimbo za Maliro.


Akulu ndi ang'onong'ono adzafa m'dziko muno; sadzaikidwa, anthu sadzachita maliro ao, sadzadzicheka, sadzadziyeseza adazi, chifukwa cha iwo;


Usa moyo mosamveka, usalira wakufayo, dzimangire chilemba, nuvale nsapato kumapazi ako, usaphimbe milomo yako. Kapena kudya mkate wa anthu.


Ndi kuti, Tinakulizirani inu zitoliro, ndipo inu simunavine; tinabuma maliro, ndipo inu simunalire.


Angofanana ndi ana akukhala pamsika, ndi kuitanizana wina ndi mnzake, ndi kunena, Ife tinakulizirani chitoliro, ndipo inu simunavine ai; tinabuma maliro, ndimo simunalire ai.


Ndipo potsikirako Paulo, anamgwera namfungatira, nati, Musachite phokoso, pakuti moyo wake ulipo.


Ndipo Petro ananyamuka, napita nao. M'mene anafikako, anapita naye kuchipinda chapamwamba; ndipo amasiye onse anaimirirapo pali iye, nalira, namuonetsa malaya ndi zovala zimene Dorika adasoka, pamene anali nao pamodzi.


Ndipo mau a anthu oimba zeze, ndi a oimba, ndi a oliza zitoliro, ndi a oomba malipenga sadzamvekanso konse mwa iwe; ndipo mmisiri aliyense wa machitidwe ali onse sadzapezedwanso konse mwa iwe; ndi mau a mphero sadzamvekanso konse mwa iwe;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa