Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Masalimo 2:5 - Buku Lopatulika

Pomwepo adzalankhula nao mu mkwiyo wake, nadzawaopsa mu ukali wake.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Pomwepo adzalankhula nao mu mkwiyo wake, nadzawaopsa m'ukali wake.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tsono adzaŵadzudzula ali wokwiya adzaŵaopseza ali wokalipa.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ndipo iye awadzudzula mu mkwiyo wake ndi kuwaopseza mu ukali wake, kunena kuti,

Onani mutuwo



Masalimo 2:5
15 Mawu Ofanana  

Ichi chikhale mphotho ya otsutsana nane yowapatsa Yehova, ndi ya iwo akunenera choipa moyo wanga.


Mudzawaika ngati ng'anjo yamoto pa nyengo ya mkwiyo wanu. Yehova adzawatha m'kukwiya kwake, ndipo moto udzawanyeketsa.


koma ndi chilungamo adzaweruza aumphawi, nadzadzudzulira ofatsa a m'dziko moongoka; ndipo adzamenya dziko lapansi ndi chibonga cha kukamwa kwake, nadzapha oipa ndi mpweya wa milomo yake.


Pakuti Yehova akwiyira amitundu onse, nachitira ukali khamu lao lonse; Iye wawaononga psiti, wawapereka kukaphedwa.


Mau a phokoso achokera m'mzinda, mau ochokera mu Kachisi, mau a Yehova amene abwezera adani ake chilango.


Ndipo ndikwiya nao amitundu okhala osatekeseka ndi mkwiyo waukulu; pakuti ndinakwiya pang'ono, ndipo anathandizira choipa.


Koma mfumu inakwiya; nituma asilikali ake napululutsa ambanda aja, nitentha mzinda wao.


Koma adani anga aja osafuna kuti ndidzakhala mfumu yao, bwerani nao kuno, nimuwaphe pamaso panga.


Ndipo m'dzanja lake lamanja munali nyenyezi zisanu ndi ziwiri; ndi m'kamwa mwake mudatuluka lupanga lakuthwa konsekonse; ndipo nkhope yake ngati dzuwa lowala mu mphamvu yake.


Ndipo m'kamwa mwake mutuluka lupanga lakuthwa, kuti akanthe nalo mitundu ya anthu; ndipo Iye adzawalamulira ndi ndodo yachitsulo: ndipo aponda Iye moponderamo mphesa mwa vinyo waukali wa mkwiyo wa Mulungu Wamphamvuyonse.