Wakhazikika mtima wanga, Mulungu; ndidzaimba, inde ndidzaimba zolemekeza, ndiko ulemerero wanga.
Masalimo 16:9 - Buku Lopatulika Chifukwa chake wasekera mtima wanga, nukondwera ulemu wanga; mnofu wanganso udzakhala mokhazikika. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake wasekera mtima wanga, nukondwera ulemu wanga; mnofu wanganso udzakhala mokhazikika. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nchifukwa chake mtima wanga ukukondwa, ndipo m'katikati mwangamu ndikusangalala. Thupi langanso lidzakhala pabwino, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho mtima wanga ndi wosangalala ndipo pakamwa panga pakukondwera; thupi langanso lidzakhala pabwino, |
Wakhazikika mtima wanga, Mulungu; ndidzaimba, inde ndidzaimba zolemekeza, ndiko ulemerero wanga.
kuti ulemu wanga uimbire Inu, wosakhala chete. Yehova Mulungu wanga, ndidzakuyamikani nthawi zonse.
Akufa anu adzakhala ndi moyo; mitembo yao idzauka. Ukani muimbe, inu amene mukhala m'fumbi; chifukwa mame ako akunga mame a pamasamba, ndipo dziko lapansi lidzatulutsa mizimu.
Koma iwe, muka mpaka chimaliziro; pakuti udzapumula, nudzaima m'gawo lako masiku otsiriza.
mwa ichi unakondwera mtima wanga, ndipo linasangalala lilime langa; ndipo thupi langanso lidzakhala m'chiyembekezo.