Nati iye, Akapanda kukuthandiza Yehova, ndikaona kuti kokuthandiza ine? Kudwale kodi, kapena popondera mphesa?
Masalimo 146:3 - Buku Lopatulika Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Musakhulupirire mafumu kapena anthu ena amene sangathe kuthandiza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Musamadalire mafumu, anthu osakhalitsa, amene sangathe kupulumutsa. |
Nati iye, Akapanda kukuthandiza Yehova, ndikaona kuti kokuthandiza ine? Kudwale kodi, kapena popondera mphesa?
Nthawi yomweyi Hanani mlauli anadza kwa Asa mfumu ya Yuda, nanena naye, Popeza mwatama mfumu ya Aramu, osatama Yehova Mulungu wanu, chifukwa chake khamu la nkhondo la mfumu ya Aramu lapulumuka m'dzanja lanu.
Indetu, anthu achabe ndi mpweya, ndipo anthu aakulu ndi bodza, pakuwayesa apepuka; onse pamodzi apepuka koposa mpweya.
Siyani munthu, amene mpweya wake uli m'mphuno mwake; chifukwa m'mene awerengedwamo ndi muti?
Tsiku limenelo, ati Yehova wa makamu, chikhomo chokhomeredwa polimba udzasukusika; nudzaguluka, ndi kugwa, ndi katundu wopachikidwapo adzadulidwa; pakuti Yehova wanena.
Koma Aejipito ndiwo anthu, si Mulungu; ndi akavalo ao ali nyama, si mzimu; ndipo pamene Yehova adzatambasula dzanja lake, wothandiza adzaphunthwa, ndi wothandizidwa adzagwa, ndipo iwo onse awiri pamodzi adzalephera.
Ndipo Yesaya anati kwa iwo, Mukati kwa mbuyanu, Atero Yehova, musaope mau amene wawamva iwe, amene atumiki a mfumu ya Asiriya andilalatira Ine.