Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 16:7 - Buku Lopatulika

7 Nthawi yomweyi Hanani mlauli anadza kwa Asa mfumu ya Yuda, nanena naye, Popeza mwatama mfumu ya Aramu, osatama Yehova Mulungu wanu, chifukwa chake khamu la nkhondo la mfumu ya Aramu lapulumuka m'dzanja lanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Nthawi yomweyi Hanani mlauli anadza kwa Asa mfumu ya Yuda, nanena naye, Popeza mwatama mfumu ya Aramu, osatama Yehova Mulungu wanu, chifukwa chake khamu la nkhondo la mfumu ya Aramu lapulumuka m'dzanja lanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Nthaŵi imeneyo mneneri Hanani adadza kwa Asa mfumu ya ku Yuda, namuuza kuti, “Chifukwa chakuti mudakhulupirira mfumu ya ku Siriya, osakhulupirira Chauta, Mulungu wanu, gulu lankhondo la mfumu ya ku Siriya lakuthaŵirani.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Nthawi imeneyi mlosi Hanani anabwera kwa Asa mfumu ya Yuda ndipo anati kwa iye, “Chifukwa chakuti munadalira mfumu ya Aramu osati Yehova Mulungu wanu, gulu la ankhondo la mfumu ya ku Aramu lapulumuka mʼmanja mwanu.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 16:7
19 Mawu Ofanana  

Pakhale pangano pakati pa ine ndi inu, pakati pa atate wanga ndi atate wanu; taonani, ndatumiza kwa inu mphatso ya siliva ndi golide, tiyeni lilekeke pangano lili pakati pa inu ndi Baasa mfumu ya Israele, kuti andichokere.


Ndipo mau a Yehova akutsutsa Baasa anadza kwa Yehu mwana wa Hanani, nati,


Ndiponso mau a Yehova anadza ndi dzanja la mneneri Yehu mwana wa Hanani, kutsutsa Baasa ndi nyumba yake, chifukwa cha zoipa zonse anazichita iye pamaso pa Yehova; popeza anaputa mkwiyo wake ndi machitidwe a manja ake, nafanana ndi nyumba ya Yerobowamu; ndiponso popeza anaikantha.


Anakhulupirira Yehova Mulungu wa Israele; atafa iye panalibe wakunga iye mwa mafumu onse a Yuda, ngakhale mwa iwo okhalapo asanabadwe iye.


Ndipo anathandizidwa polimbana nao; ndi Ahagiri anaperekedwa m'dzanja lao, ndi onse anali nao; pakuti anafuulira kwa Mulungu pomenyana nao, ndipo anapembedzeka nao, popeza anamkhulupirira Iye.


Momwemo anachepetsedwa ana a Israele nthawi ija, napambana ana a Yuda; popeza anatama Yehova Mulungu wa makolo ao.


Ndipo Asa anafuulira kwa Yehova Mulungu wake, nati, Yehova, palibe wina ngati Inu, kuthandiza pakati pa wamphamvu ndi iye wopanda mphamvu; tithandizeni Yehova Mulungu wathu, titama Inu, tatulukira aunyinji awa m'dzina lanu. Yehova, Inu ndinu Mulungu wathu, munthu asakukanikeni.


Pamenepo Asa mfumu anatenga Ayuda onse, ndipo anatuta miyala ya ku Rama, ndi mitengo yake, imene Baasa adamanga nayo, namangira Geba ndi Mizipa.


Natuluka Yehu mwana wa Hanani mlauli kukomana naye, nati kwa mfumu Yehosafati, Muyenera kodi kuthandiza zoipa, ndi kukonda amene adana ndi Yehova? Chifukwa cha ichi ukugwerani mkwiyo wochokera kwa Yehova.


Ndipo anayenda m'njira ya Asa atate wake osapatukamo, nachita zoongoka pamaso pa Yehova.


Machitidwe ena tsono adazichita Yehosafati, zoyamba ndi zotsiriza, taonani, zilembedwa m'buku la mau a Yehu mwana wa Hanani, wotchulidwa m'buku la mafumu a Israele.


Pakuti khamu la nkhondo la Aaramu linadza la anthu owerengeka; ndipo Yehova anapereka khamu lalikulu m'dzanja lao; popeza adasiya Yehova Mulungu wa makolo ao. Motero anachitira Yowasi zomlanga.


Tsoka kwa iwo amene atsikira kunka ku Ejipito kukathandizidwa, natama akavalo; nakhulupirira magaleta, pakuti ali ambiri, ndi okwera pa akavalo, pakuti ali a mphamvu zambiri; koma sayang'ana Woyera wa Israele, ngakhale kumfuna Yehova!


Ndipo munthu adzakhala monga pobisalira mphepo, ndi pousira chimphepo; monga mitsinje yamadzi m'malo ouma, monga mthunzi wa thanthwe lalikulu m'dziko lotopetsa.


Ndipo anadza Yesaya mneneri kwa mfumu Hezekiya, nati kwa iye, Kodi anthu awa ananena bwanji, ndipo iwo achokera kuti, kudza kwa inu? Ndipo Hezekiya anati, Iwo achokera ku dziko lakutali, kudza kwa ine, kunena ku Babiloni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa