Ndidzaimbira Yehova, pakuti anandichitira zokoma.
Ndidzaimbira Chauta, popeza kuti wandichitira zabwino.
Ine ndidzayimbira Yehova pakuti wandichitira zokoma.
Ubwere moyo wanga ku mpumulo wako; pakuti Yehova anakuchitira chokoma.
Ndidzakuyamikani ndi mtima woongoka, pakuphunzira maweruzo anu olungama.
Kwezekani, Yehova, mu mphamvu yanu; potero tidzaimba ndi kulemekeza chilimbiko chanu.
Yehova ndiye mphamvu yanga, ndi chikopa changa; mtima wanga wakhulupirira Iye, ndipo anandithandiza, chifukwa chake mtima wanga ukondwera kwakukulu; ndipo ndidzamyamika nayo nyimbo yanga.
Amitundu anagwa m'mbuna imene anaikumba, lakodwa phazi lao muukonde anautchera.