Masalimo 13:1 - Buku Lopatulika Mudzandiiwala chiiwalire, Yehova, kufikira liti? Mudzandibisira ine nkhope yanu kufikira liti? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mudzandiiwala chiiwalire, Yehova, kufikira liti? Mudzandibisira ine nkhope yanu kufikira liti? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kodi mpaka liti, Inu Chauta? Kodi mudzandiiŵala mpaka muyaya? Kodi mudzandibisira nkhope yanu nthaŵi zonse? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mpaka liti Yehova? Kodi mudzandiyiwala mpaka kalekale? Mpaka liti mudzandibisira nkhope yanu? |
Ambuye, mudzapenyererabe nthawi yanji? Bwezani moyo wanga kwa zakundiononga zao, wanga wa wokha kwa misona ya mkango.
Mudzabisala kosatha kufikira liti, Yehova; ndi kuzaza kwanu kudzatentha ngati moto kufikira liti?
Mutikhutitse nacho chifundo chanu m'mawa; ndipo tidzafuula mokondwera ndi kukondwera masiku athu onse.
koma zoipa zanu zakulekanitsani inu ndi Mulungu wanu; ndipo machimo anu abisa nkhope yake kwa inu, kuti Iye sakumva.
Pamenepo ndidzawapsera mtima tsiku ilo, ndipo ndidzawataya, ndi kuwabisira nkhope yanga, ndipo adzathedwa, ndi zoipa ndi zovuta zambiri zidzawafikira; kotero kuti adzati tsiku lija, Sizitifikira kodi zoipa izi popeza Mulungu wathu sakhala pakati pa ife?