Masalimo 101:5 - Buku Lopatulika Wakuneneza mnzake m'tseri ndidzamdula; wa maso odzikuza ndi mtima wodzitama sindidzamlola. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Wakuneneza mnzake m'tseri ndidzamdula; wa maso odzikuza ndi mtima wodzitama sindidzamlola. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Munthu wosinjirira mnzake kuseri ndidzamcheteketsa. Wooneka wonyada ndi wodzikuza sindidzamulekerera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Aliyense wosinjirira mnansi wake mseri ameneyo ndidzamuletsa; aliyense amene ali ndi maso amwano ndi mtima wodzikuza, ameneyo sindidzamulekerera. |
Amene sasinjirira ndi lilime lake, nachitira mnzake choipa, ndipo satola miseche pa mnansi wake.
Usatola mbiri yopanda pake; usathandizana naye woipa ndi kukhala mboni yochititsa chiwawa.
Maso a munthu akuyang'anira kumwamba adzatsitsidwa, ndi kudzikweza kwa anthu kudzaweramitsidwa pansi; ndipo Yehova yekha adzakwezedwa tsiku limenelo.
Anthu oneneza anali mwa iwe, kuti akhetse mwazi; ndipo anadya pamapiri mwa iwe, pakati pa iwe anachita zamanyazi.
Tsono ine Nebukadinezara ndiyamika, ndi kukuza, ndi kulemekeza Mfumu ya Kumwamba, pakuti ntchito zake zonse nzoona, ndi njira zake chiweruzo; ndi oyenda m'kudzikuza kwao, Iye akhoza kuwachepetsa.
Usamayendayenda nusinjirira mwa anthu a mtundu wako; usamatsata mwazi wa mnansi wako; Ine ndine Yehova.
Ndinena ndi inu, anatsikira kunyumba kwake woyesedwa wolungama uyutu, wosati uja ai; pakuti yense wakudzikuza yekha adzachepetsedwa; koma wodzichepetsa yekha adzakulitsidwa.
koma tsopano ndalembera inu kuti musayanjane naye, ngati wina wotchedwa mbale ali wachigololo, kapena wosirira, kapena wopembedza mafano, kapena wolalatira, kapena woledzera, kapena wolanda, kungakhale kukadya naye wotere, iai.
Momwemonso akazi okalamba akhale nao makhalidwe oyenera anthu oyera, osadierekeza, osakodwa nacho chikondi cha pavinyo, akuphunzitsa zokoma;
Musalankhulenso modzikuza kwambiri motero; m'kamwa mwanu musatuluke zolulutsa; chifukwa Yehova ndi Mulungu wanzeru, ndipo Iye ayesa zochita anthu.