Masalimo 101:1 - Buku Lopatulika Ndidzaimba zachifundo ndi chiweruzo; ndidzaimba zakukulemekezani Inu, Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndidzaimba zachifundo ndi chiweruzo; ndidzaimba zakukulemekezani Inu, Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndidzaimba nyimbo zotamanda kukhulupirika ndi kulungama. Ndidzakuimbirani Inu Chauta. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndidzayimba za chikondi ndi chiweruzo chanu cholungama; kwa Inu Yehova ndidzayimba matamando. |
Mundilanditse kumlandu wa mwazi, Mulungu, ndinu Mulungu wa chipulumutso changa; lilime langa lidzakweza nyimbo ya chilungamo chanu.
Ndidzaimbira zachifundo za Yehova nthawi yonse, pakamwa panga ndidzadziwitsira chikhulupiriko chanu ku mibadwomibadwo.
Ziyoni anamva nakondwera, nasekerera ana aakazi a Yuda; chifukwa cha maweruzo anu, Yehova.
Iye anakuuza, munthuwe, chomwe chili chokoma; ndipo Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.
Chifukwa chake onani kukoma mtima ndi kuuma mtima kwake kwa Mulungu: kwa iwo adagwa, kuuma kwake; koma kwa iwe kukoma mtima kwake kwa Mulungu, ngati ukhala chikhalire m'kukoma mtimamo; koma ngati sutero, adzakusadza iwe.