Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 89:1 - Buku Lopatulika

1 Ndidzaimbira zachifundo za Yehova nthawi yonse, pakamwa panga ndidzadziwitsira chikhulupiriko chanu ku mibadwomibadwo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndidzaimbira zachifundo za Yehova nthawi yonse, pakamwa panga ndidzadziwitsira chikhulupiriko chanu ku mibadwomibadwo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Inu Chauta, ndidzaimba mosalekeza nyimbo yotamanda chikondi chanu chosasinthika. Ndidzalalika ndi pakamwa panga za kukhulupirika kwanu ku mibadwo yonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Ndidzayimba za chikondi chachikulu cha Yehova kwamuyaya; ndi pakamwa panga ndidzachititsa kuti kukhulupirika kwanu kudziwike ku mibado yonse.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 89:1
24 Mawu Ofanana  

Pakuti anali wanzeru woposa anthu onse, woposa Etani wa ku Ezara, ndi Hemani, ndi Kalikoli, ndi Darida ana a Maholi; ndipo mbiri yake inafikira amitundu onse ozungulira.


Ndipo Solomoni anapatsa Hiramu miyeso ya tirigu zikwi makumi awiri ndiyo zakudya za banja lake, ndi miyeso makumi awiri ya mafuta oyera; motero Solomoni anapatsa Hiramu chaka ndi chaka.


Ndi ana a Zera: Zimiri, ndi Etani, ndi Hemani, ndi Kalikoli, ndi Dara; onse pamodzi ndi asanu.


Ndidzaimba zachifundo ndi chiweruzo; ndidzaimba zakukulemekezani Inu, Yehova.


Aleluya. Yamikani Yehova; pakuti Iye ndiye wabwino: Pakuti chifundo chake nchosatha.


Chikhulupiriko chanu chifikira mibadwomibadwo; munakhazikitsa dziko lapansi, ndipo likhalitsa.


Yehova, m'mwamba muli chifundo chanu; choonadi chanu chifikira kuthambo.


Koma ine, ndidzaimbira mphamvu yanu; inde ndidzaimbitsa chifundo chanu mamawa, pakuti Inu mwakhala msanje wanga, ndi pothawirapo ine tsiku la nsautso yanga.


M'kamwa mwanga mudzadzala lemekezo lanu, ndi ulemu wanu tsiku lonse.


Adzafotokozera chifundo chanu kumanda kodi, chikhulupiriko chanu kumalo a chionongeko?


Koma chikhulupiriko changa ndi chifundo changa zidzakhala naye; ndipo nyanga yake idzakwezeka m'dzina langa.


Koma sindidzamchotsera chifundo changa chonse, ndi chikhulupiriko changa sichidzamsowa.


Chilikuti chifundo chanu chakale, Ambuye, munachilumbirira Davide pa chikhulupiriko chanu?


Yehova, Mulungu wa makamu, wamphamvu ndani wonga Inu, Yehova? Ndipo chikhulupiriko chanu chikuzingani.


Kuonetsera chifundo chanu mamawa, ndi chikhulupiriko chanu usiku uliwonse.


Yehova, Inu ndinu Mulungu wanga, ndidzakukuzani Inu, ndidzatamanda dzina lanu, chifukwa mwachita zinthu zodabwitsa, ngakhale zauphungu zakale, mokhulupirika ndi m'zoonadi.


chioneka chatsopano m'mawa ndi m'mawa; mukhulupirika ndithu.


Mudzapatsa kwa Yakobo choonadi, ndi kwa Abrahamu chifundo chimene munalumbirira makolo athu kuyambira masiku a kale lomwe.


m'chiyembekezo cha moyo wosatha, umene Mulungu, wosanamayo, analonjeza zisanayambe nthawi zosayamba;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa