Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Marko 7:4 - Buku Lopatulika

ndipo pakuchoka kumsika, sakudya osasamba m'thupi; ndipo zilipo zinthu zina zambiri anazilandira kuzisunga, ndizo matsukidwe a zikho, ndi miphika, ndi zotengera zamkuwa.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

ndipo pakuchoka kumsika, sakudya osasamba m'thupi; ndipo zilipo zinthu zina zambiri anazilandira kuzisunga, ndizo matsukidwe a zikho, ndi miphika, ndi zotengera zamkuwa.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ndipo akachokera ku msika, saadya osasamba m'manja. Amasunganso miyambo ina yambiri imene makolo ao adaŵasiyira, monga kutsuka zikho, miphika, ndi ziŵiya zamkuŵa [ndi mabedinso.]

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Akabwera kuchokera ku msika samadya pokhapokha atasamba. Ndipo amasunga miyambo ina yambiri monga, kutsuka zikho, mitsuko ndi maketulo).

Onani mutuwo



Marko 7:4
15 Mawu Ofanana  

Ndidzasamba manja anga mosalakwa; kuti ndizungulire guwa la nsembe lanu, Yehova;


Sambani, dziyeretseni; chotsani machitidwe anu oipa pamaso panga; lekani kuchita zoipa;


ndipo ndinaika pamaso pa ana aamuna a nyumba ya Arekabu mbale zodzala ndi vinyo, ndi zikho, ndipo ndinati kwa iwo, Imwani vinyo.


Iwe Yerusalemu, utsuke mtima wako kuchotsa zoipa kuti upulumuke. Maganizo ako achabe agona mwako masiku angati?


Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mutsuka kunja kwake kwa chikho ndi mbale, koma m'katimo iwo adzala ndi kulanda ndi kusadziletsa.


Mfarisi iwe wakhungu, yambawatsuka m'kati mwa chikho ndi mbale, kuti kunja kwake kukhalenso koyera.


Koma Pilato poona kuti sanafitse, koma kuti linapambana phokoso, anatenga madzi, nasamba manja pamaso pa khamulo, nati, Ine ndilibe kuchimwira mwazi wa munthu uyu wolungama, mudzionere nokha.


Musiya lamulo la Mulungu, nimusunga mwambo wa anthu.


Ndipo panali pamenepo mitsuko yamiyala isanu ndi umodzi yoikidwako monga mwa mayeretsedwe a Ayuda, yonse ya miyeso iwiri kapena itatu.


Pamenepo padauka kufunsana mwa ophunzira ake a Yohane ndi Myuda za mayeretsedwe.


Popeza akhala zoikika za thupi zokha (ndi zakudya, ndi zakumwa, ndi masambidwe osiyanasiyana), oikidwa kufikira nthawi yakukonzanso.


Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu. Sambani m'manja, ochimwa inu; yeretsani mitima, a mitima iwiri inu.


koma ngati tiyenda m'kuunika, monga Iye ali m'kuunika, tiyanjana wina ndi mnzake, ndipo mwazi wa Yesu Mwana wake utisambitsa kutichotsera uchimo wonse.