Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 23:26 - Buku Lopatulika

26 Mfarisi iwe wakhungu, yambawatsuka m'kati mwa chikho ndi mbale, kuti kunja kwake kukhalenso koyera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Mfarisi iwe wakhungu, yambotsuka m'kati mwa chikho ndi mbale, kuti kunja kwake kukhalenso koyera.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 Afarisi akhungu inu, yambani mwatsuka m'kati mwa chikho, ndipo kunja kwakenso kudzayera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 Afarisi akhungu! Poyamba tsukani mʼkati mwa chikho ndi mbale, ndipo kunja kwake kudzakhalanso koyera.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 23:26
12 Mawu Ofanana  

woipa asiye njira yake, ndi munthu wosalungama asiye maganizo ake, nabwere kwa Yehova; ndipo Yehova adzamchitira chifundo; ndi kwa Mulungu wathu, pakuti Iye adzakhululukira koposa.


Ndaona zonyansa zako, ndi zigololo zako, ndi zakumemesa zako, ndi chinyerinyeri cha dama lako, pamapiri ndi m'munda. Tsoka kwa iwe, Yerusalemu! Sudzayeretsedwa; kodi zidzatero mpaka liti?


Iwe Yerusalemu, utsuke mtima wako kuchotsa zoipa kuti upulumuke. Maganizo ako achabe agona mwako masiku angati?


Tayani, ndi kudzichotsera zolakwa zanu zonse zimene munalakwa nazo, ndi kudzifunira mtima watsopano, ndi mzimu watsopano; pakuti mudzaferanji inu, nyumba ya Israele?


Ukakoma mtengo, chipatso chake chomwe chikoma; ukaipa mtengo, chipatso chake chomwe chiipa; pakuti ndi chipatso chake mtengo udziwika.


Ndipo iye, atampangira amake, anati, Ndipatseni ine kuno m'mbale mutu wa Yohane Mbatizi.


ndipo pakuchoka kumsika, sakudya osasamba m'thupi; ndipo zilipo zinthu zina zambiri anazilandira kuzisunga, ndizo matsukidwe a zikho, ndi miphika, ndi zotengera zamkuwa.


Koma Ambuye anati kwa iye, Tsopano inu Afarisi muyeretsa kunja kwake kwa chikho ndi mbale, koma m'kati mwanu mudzala zolanda ndi zoipa.


Munthu wabwino atulutsa zabwino m'chuma chokoma cha mtima wake; ndi munthu woipa atulutsa zoipa m'choipa chake: pakuti m'kamwa mwake mungolankhula mwa kuchuluka kwa mtima wake.


Pokhala nao tsono malonjezano amenewa, okondedwa, tidzikonzere tokha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu, ndi kutsiriza chiyero m'kuopa Mulungu.


tiyandikire ndi mtima woona, m'chikhulupiriro chokwanira, ndi mitima yathu yowazidwa kuichotsera chikumbumtima choipa, ndi matupi athu osambitsidwa ndi madzi oyera;


Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu. Sambani m'manja, ochimwa inu; yeretsani mitima, a mitima iwiri inu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa