Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 23:27 - Buku Lopatulika

27 Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mufanafana ndi manda opaka njereza, amene aonekera okoma kunja kwake, koma adzala m'katimo ndi mafupa a anthu akufa ndi zonyansa zonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mufanafana ndi manda opaka njereza, amene aonekera okoma kunja kwake, koma adzala m'katimo ndi mafupa a anthu akufa ndi zonyansa zonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 “Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Muli ngati manda opaka njeresa, amene amaoneka okongola kunja, pamene m'kati mwake m'modzaza ndi mafupa a anthu akufa ndi zoola zina zilizonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 “Tsoka kwa inu, aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi, achiphamaso! Muli ngati ziliza pa manda zowala kunja zimene zimaoneka zokongola koma mʼkatimo mwadzaza mafupa a anthu akufa ndi zonyansa zina zonse.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 23:27
7 Mawu Ofanana  

Milomo yofunitsitsa ndi mtima woipa ikunga mbale yadothi anaimata ndi mphala ya siliva.


Ndipo aliyense wakukhudza munthu wophedwa ndi lupanga, kapena mtembo, kapena fupa la munthu, kapena manda, pathengo poyera, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri.


Chomwecho inunso muonekera olungama pamaso pa anthu, koma m'kati muli odzala ndi chinyengo ndi kusaweruzika.


Tsoka inu! Chifukwa muli ngati manda osaoneka, ndipo anthu akuyendayenda pamwamba pao sadziwa.


Pamenepo Paulo anati kwa iye, Mulungu adzakupanda iwe, khoma loyeretsedwa iwe; ndipo kodi ukhala iwe wakundiweruza mlandu monga mwa chilamulo, ndipo ulamulira andipande ine posanga chilamulo?


Onse amene afuna kuonekera okoma m'thupi, iwowa akukakamizani inu mudulidwe; chokhacho, chakuti angazunzike chifukwa cha mtanda wa Khristu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa