Ndipo muziidya chotero: okwinda m'chuuno, nsapato zanu pa mapazi anu ndodo yanu m'dzanja lanu, ndipo muziidya msanga; ndiye Paska wa Yehova.
Luka 2:41 - Buku Lopatulika Ndipo atate wake ndi amake akamuka chaka ndi chaka ku Yerusalemu ku Paska. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo atate wake ndi amake akamuka chaka ndi chaka ku Yerusalemu ku Paska. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Makolo a Yesu ankapita ku Yerusalemu chaka ndi chaka ku chikondwerero cha Paska. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Chaka chilichonse makolo ake ankapita ku Yerusalemu ku phwando la Paska. |
Ndipo muziidya chotero: okwinda m'chuuno, nsapato zanu pa mapazi anu ndodo yanu m'dzanja lanu, ndipo muziidya msanga; ndiye Paska wa Yehova.
Ndipo tsiku lino lidzakhala kwa inu chikumbutso, muzilisunga la chikondwerero cha Yehova; ku mibadwo yanu muzilisunga la chikondwerero, likhale lemba losatha.
Amuna ako onse azioneka pamaso pa Yehova Mulungu, Mulungu wa Israele, katatu chaka chimodzi.
Ndipo pamene Iye anakhala ndi zaka zake khumi ndi ziwiri, anakwera iwo monga machitidwe a chikondwerero;
Koma Paska wa Ayuda anali pafupi; ndipo ambiri anakwera kunka ku Yerusalemu kuchoka kuminda, asanafike Paska, kukadziyeretsa iwo okha.
Koma pasanafike chikondwerero la Paska, Yesu, podziwa kuti nthawi yake idadza yakuchoka kutuluka m'dziko lino lapansi, kunka kwa Atate, m'mene anakonda ake a Iye yekha a m'dziko lapansi, anawakonda kufikira chimaliziro.
Pamenepo padzakhala malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lake, kumeneko muzibwera nazo zonse ndikuuzanizi; nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zanu zophera, magawo anu onse a magawo khumi, ndi nsembe yokweza dzanja lanu, ndi zowinda zanu zosankhika zimene muzilonjezera Yehova.
koma muzizidya pamaso pa Yehova Mulungu wanu m'malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha, inu, ndi ana anu aamuna, ndi ana anu aakazi, ndi antchito anu aamuna, ndi antchito anu aakazi, ndi Mlevi ali m'mudzi mwanu; nimukondwere pamaso pa Yehova Mulungu wanu m'zonse mudazigwira ndi dzanja lanu.
Amuna onse azioneka pamaso pa Yehova Mulungu wanu m'malo amene Iye adzasankha, katatu m'chaka; pa chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa, pa chikondwerero cha masabata, ndi pa chikondwerero cha Misasa; ndipo asaoneke pamaso pa Yehova opanda kanthu;
Ndipo munthuyo Elikana, ndi a pa banja lake onse, anakwera kukapereka kwa Yehova nsembe ya chaka ndi chaka, ndi ya chowinda chake.
Ndipo munthuyo akakwera chaka ndi chaka kutuluka m'mzinda mwake kukalambira ndi kupereka nsembe kwa Yehova wa makamu mu Silo. Ndipo pomwepo panali ana aamuna awiri a Eli, ansembe a Yehova, ndiwo Hofeni ndi Finehasi.