Ndipo ana analimbana m'kati mwake: ndipo iye anati, Ngati chotero, ine ndikhala ndi moyo bwanji? Ndipo ananka kukafunsa kwa Yehova.
Luka 1:41 - Buku Lopatulika Ndipo panali pamene Elizabeti anamva kulonjera kwake kwa Maria, mwana wosabadwayo anatsalima m'mimba mwake; ndipo Elizabeti anadzazidwa ndi Mzimu Woyera; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo panali pamene Elizabeti anamva kulonjera kwake kwa Maria, mwana wosabadwayo anatsalima m'mimba mwake; ndipo Elizabeti anadzazidwa ndi Mzimu Woyera; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene Elizabeti adamva malonje a Maria, mwana adayamba kutakataka m'mimba mwake. Elizabeti adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Elizabeti atamva moni wa Mariya, mwana anatakataka mʼmimba mwake, ndipo Elizabeti anadzazidwa ndi Mzimu Woyera. |
Ndipo ana analimbana m'kati mwake: ndipo iye anati, Ngati chotero, ine ndikhala ndi moyo bwanji? Ndipo ananka kukafunsa kwa Yehova.
Pakuti iye adzakhala wamkulu pamaso pa Ambuye, ndipo sadzamwa konse vinyo kapena kachasu; nadzadzazidwa ndi Mzimu Woyera, kuyambira asanabadwe.
nakweza mau ndi mfuu waukulu, nati, Wodalitsika iwe mwa akazi, ndipo chodalitsika chipatso cha mimba yako.
Pakuti ona, pamene mau a moni wako analowa m'makutu anga, mwana anatsalima ndi msangalalo m'mimba mwanga.
Ndipo Yesu, wodzala ndi Mzimu Woyera, anabwera kuchokera ku Yordani, natsogozedwa ndi Mzimu kunka kuchipululu
Ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula ndi malilime ena, monga Mzimu anawalankhulitsa.
Pamenepo Petro, wodzala ndi Mzimu Woyera anati kwa iwo, Oweruza a anthu inu, ndi akulu,
Chifukwa chake, abale, yang'anani mwa inu amuna asanu ndi awiri a mbiri yabwino, odzala ndi Mzimu ndi nzeru, amene tikawaike asunge ntchito iyi.
Koma iye, pokhala wodzala ndi Mzimu Woyera, anapenyetsetsa Kumwamba, naona ulemerero wa Mulungu, ndi Yesu alikuimirira padzanja lamanja la Mulungu,
Ndipo anachoka Ananiya, nalowa m'nyumbayo; ndipo anaika manja ake pa iye, nati, Saulo, mbale, Ambuye wandituma ine, ndiye Yesu amene anakuonekerani panjira wadzerayo, kuti upenyenso, ndi kudzazidwa ndi Mzimu Woyera.
Ndinagwidwa ndi Mzimu tsiku la Ambuye, ndipo ndinamva kumbuyo kwanga mau aakulu, ngati a lipenga,