Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 7:55 - Buku Lopatulika

55 Koma iye, pokhala wodzala ndi Mzimu Woyera, anapenyetsetsa Kumwamba, naona ulemerero wa Mulungu, ndi Yesu alikuimirira padzanja lamanja la Mulungu,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

55 Koma iye, pokhala wodzala ndi Mzimu Woyera, anapenyetsetsa Kumwamba, naona ulemerero wa Mulungu, ndi Yesu alikuimirira pa dzanja lamanja la Mulungu,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

55 Koma Stefano, atadzazidwa ndi Mzimu Woyera, adayang'ana kumwamba naona ulemerero wa Mulungu, ndiponso Yesu ataimirira ku dzanja lamanja la Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

55 Koma Stefano, wodzaza ndi Mzimu Woyera, anayangʼana kumwamba ndipo anaona ulemerero wa Mulungu ndiponso Yesu atayimirira ku dzanja lamanja la Mulungu.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 7:55
27 Mawu Ofanana  

Popeza adzaima padzanja lamanja la waumphawi, kumpulumutsa kwa iwo akuweruza koipa moyo wake.


Ndipo ulemerero wa Yehova unachoka pa chiundo cha nyumba, nuima pamwamba pa akerubi.


Ndipo ulemerero wa Yehova unakwera kuchokera kukerubi kunka kuchiundo cha nyumba; ndi nyumba inadzala nao mtambo, ndi bwalo linadzala ndi cheza cha ulemerero wa Yehova.


Ndipo ulemerero wa Yehova unakwera kuchoka pakati pa mzinda, nuima paphiri la kum'mawa kwa mzinda.


Ndipo ndinauka ndi kutuluka kunka kuchidikha, ndipo taonani, ulemerero wa Yehova unaimako monga ulemerero uja ndinauona kumtsinje Kebara, ndipo ndinagwa nkhope pansi.


Koma ine ndidzala nayo mphamvu mwa Mzimu ya Yehova, ndi chiweruzo, ndi chamuna, kufotokozera Yakobo kulakwa kwake, ndi kwa Israele tchimo lake.


Pamenepo Ambuye Yesu, atatha kulankhula nao, analandiridwa Kumwamba, nakhala padzanja lamanja la Mulungu.


Pomwepo anachotsa mwala. Koma Yesu anakweza maso ake kupenya kumwamba nati, Atate, ndiyamika Inu kuti munamva Ine.


Izi anati Yesaya, chifukwa anaona ulemerero wake; nalankhula za Iye.


Ndipo ngati ndipita kukakonzera inu malo, ndidzabweranso, ndipo ndidzalandira inu kwa Ine ndekha; kuti kumene kuli Ineko, mukakhale inunso.


Ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula ndi malilime ena, monga Mzimu anawalankhulitsa.


Pamenepo Petro, wodzala ndi Mzimu Woyera anati kwa iwo, Oweruza a anthu inu, ndi akulu,


Ndipo sanathe kuipambana nzeru ndi Mzimu amene analankhula naye.


Chifukwa chake, abale, yang'anani mwa inu amuna asanu ndi awiri a mbiri yabwino, odzala ndi Mzimu ndi nzeru, amene tikawaike asunge ntchito iyi.


Ndipo mau amene anakonda unyinji wonse; ndipo anasankha Stefano, ndiye munthu wodzala ndi chikhulupiriro ndi Mzimu Woyera, ndi Filipo, ndi Prokoro, ndi Nikanore ndi Timoni, ndi Parmenasi, ndi Nikolasi, ndiye wopinduka wa ku Antiokeya:


Ndipo Stefano, wodzala ndi chisomo ndi mphamvu, anachita zozizwa ndi zizindikiro zazikulu mwa anthu.


Pakuti Mulungu amene anati, Kuunika kudzawala kutuluka mumdima, ndiye amene anawala m'mitima yathu kutipatsa chiwalitsiro cha chidziwitso cha ulemerero wa Mulungu pankhope pa Yesu Khristu.


ameneyo, pokhala ali chinyezimiro cha ulemerero wake, ndi chizindikiro chenicheni cha chikhalidwe chake, nanyamula zonse ndi mau a mphamvu yake, m'mene adachita chiyeretso cha zoipa, anakhala padzanja lamanja la Ukulu mu Mwamba,


Koma mutu wa izi tanenazi ndi uwu: Tili naye Mkulu wa ansembe wotere, amene anakhala padzanja lamanja la mpando wachifumu wa Ukulu mu Kumwamba,


Pakuti analandira kwa Mulungu Atate ulemu ndi ulemerero, pakumdzera Iye mau otere ochokera ku ulemerero waukulu, Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa, amene Ine ndikondwera naye;


ndipo unakhala nao ulemerero wa Mulungu; kuunika kwake kunafanana ndi mwala wa mtengo wake woposa, ngati mwala wayaspi, wonyezimira, ngati krustalo;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa