Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 9:17 - Buku Lopatulika

17 Ndipo anachoka Ananiya, nalowa m'nyumbayo; ndipo anaika manja ake pa iye, nati, Saulo, mbale, Ambuye wandituma ine, ndiye Yesu amene anakuonekerani panjira wadzerayo, kuti upenyenso, ndi kudzazidwa ndi Mzimu Woyera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Ndipo anachoka Ananiya, nalowa m'nyumbayo; ndipo anaika manja ake pa iye, nati, Saulo, mbale, Ambuye wandituma ine, ndiye Yesu amene anakuonekerani pa njira wadzerayo, kuti upenyenso, ndi kudzazidwa ndi Mzimu Woyera.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Pamenepo Ananiya adanyamuka nakaloŵa m'nyumbamo. Adamsanjika manja Sauloyo nati, “Mbale wanga Saulo, Ambuye Yesu amene adakuwonekera pa njira imene wadzera ija, andituma. Akufuna kuti upenyenso, ndipo udzazidwe ndi Mzimu Woyera.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Pamenepo Hananiya ananyamuka ndi kukalowa mʼnyumbayo. Anamusanjika manja Sauloyo ndipo anati, “Mʼbale Saulo, Ambuye Yesu, amene anakuonekera pa msewu pamene umabwera kuno wandituma kuti uwonenso ndi kudzazidwa ndi Mzimu Woyera.”

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 9:17
36 Mawu Ofanana  

Ndipo Yosefe anati kwa abale ake, Muyandikiretu kwa ine; nayandikira. Ndipo iye anati, Ine ndine Yosefe mbale wanu, ine ndemwe munandigulitsa ndilowe mu Ejipito.


Pamenepo anadza nato tiana kwa Iye, kuti Iye aike manja ake pa ito, ndi kupemphera: koma ophunzirawo anawadzudzula.


nanena, kuti, Kamwana kanga kabuthu kalinkutsirizika; ndikupemphani Inu mufikeko, muike manja anu pa iko, kuti kapulumuke, ndi kukhala ndi moyo.


Ndipo kumeneko sanakhoze Iye kuchita zamphamvu konse, koma kuti anaika manja ake pa anthu odwala owerengeka, nawachiritsa.


Ndipo panali pamene Elizabeti anamva kulonjera kwake kwa Maria, mwana wosabadwayo anatsalima m'mimba mwake; ndipo Elizabeti anadzazidwa ndi Mzimu Woyera;


Ndipo atate wake Zekariya anadzazidwa ndi Mzimu Woyera, nanenera za Mulungu, nati,


Eya, ndipo iwetu kamwanawe, udzanenedwa mneneri wa Wamkulukulu; pakuti udzatsogolera Ambuye, kukonza njira zake.


Koma pamene anadza mwana wanu uyu, wakutha zamoyo zanu ndi akazi achiwerewere, munamphera iye mwanawang'ombe wonenepa.


Koma kudayenera kuti tisangalale ndi kukondwerera: chifukwa mng'ono wako uyu anali wakufa ndipo ali ndi moyo; anatayika, ndipo wapezeka.


pakuti wakubadwirani inu lero, m'mzinda wa Davide, Mpulumutsi, amene ali Khristu Ambuye.


Mau amene anatumiza kwa ana a Israele, akulalikira Uthenga Wabwino wa mtendere mwa Yesu Khristu (ndiye Ambuye wa onse)


Pamenepo, m'mene adasala chakudya ndi kupemphera ndi kuika manja pa iwo, anawatumiza amuke.


Ndipo ophunzira anadzazidwa ndi chimwemwe ndi Mzimu Woyera.


Ndipo pamene Paulo anaika manja ake pa iwo, Mzimu Woyera anadza pa iwo; ndipo analankhula ndi malilime, nanenera.


Ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula ndi malilime ena, monga Mzimu anawalankhulitsa.


Ndipo pamene anazimva, analemekeza Mulungu; nati kwa iye, Uona, mbale, kuti ambirimbiri mwa Ayuda akhulupirira; ndipo ali nacho changu onsewa, cha pa chilamulo;


Ndipo ndinati, Ndinu yani Mbuye? Ndipo Ambuye anati, Ine ndine Yesu amene iwe umlondalonda.


Ndipo m'mene adapemphera iwo, panagwedezeka pamalo pamene adasonkhanirapo; ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nalankhula mau a Mulungu molimbika mtima.


amenewo anawaika pamaso pa atumwi; ndipo m'mene adapemphera, anaika manja pa iwo.


Pamenepo anaika manja pa iwo, ndipo analandira Mzimu Woyera.


Ndipo pomwepo padagwa kuchoka m'maso mwake ngati mamba, ndipo anapenyanso; ndipo ananyamuka nabatizidwa;


Chifukwa chake mulandirane wina ndi mnzake, monganso Khristu anakulandirani inu, kukachitira Mulungu ulemerero.


Munthu woyambayo ali wapansi, wanthaka. Munthu wachiwiri ali wakumwamba.


ndipo potsiriza pake pa onse, anaoneka kwa inenso monga mtayo.


Kodi sindine mfulu? Kodi sindine mtumwi? Kodi sindinaone Yesu Ambuye wathu? Kodi simuli inu ntchito yanga mwa Ambuye?


Usanyalapse mphatsoyo ili mwa iwe, yopatsidwa kwa iwe mwa chinenero, pamodzi ndi kuika kwa manja a akulu.


Usafulumira kuika manja pa munthu aliyense, kapena usayanjana nazo zoipa za eni; udzisunge wekha woyera mtima.


Chifukwa chake ndikukumbutsa iwe ukoleze mphatso ya Mulungu, ili mwa iwe mwa kuika kwa manja anga.


osatinso monga kapolo, koma woposa kapolo, mbale wokondedwa, makamaka ndi ine, koma koposa nanga ndi iwe, m'thupi, ndiponso mwa Ambuye.


a chiphunzitso cha ubatizo, a kuika manja, a kuuka kwa akufa, ndi a chiweruziro chosatha.


Ndipo yesani kulekerera kwa Ambuye wathu chipulumutso; monganso mbale wathu wokondedwa Paulo, monga mwa nzeru zopatsidwa kwa iye, anakulemberani;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa