koma mwayenda m'njira ya mafumu a Israele, ndi kuchititsa Yuda ndi okhala mu Yerusalemu chigololo, monga umo anachitira chigololo a nyumba ya Ahabu, mwaphanso abale anu a nyumba ya atate wanu, ndiwo abwino akuposa inu;
Hoseya 1:2 - Buku Lopatulika Chiyambi cha kunena kwa Yehova mwa Hoseya. Ndipo Yehova anati kwa Hoseya, Muka, udzitengere mkazi wachigololo ndi ana achigololo; pakuti dziko latsata chigololo chokhachokha kuleka kutsata Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chiyambi cha kunena kwa Yehova mwa Hoseya. Ndipo Yehova anati kwa Hoseya, Muka, udzitengere mkazi wachigololo ndi ana achigololo; pakuti dziko latsata chigololo chokhachokha kuleka kutsata Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene Chauta adalankhula koyamba kudzera mwa Hoseya, adamuuza kuti, “Pita kakwatire mkazi wachiwerewere ndipo ubale naye ana omwe adzakhalenso achiwerewere. Pakuti anthu a m'dziko muno akhala osakhulupirika, pakusiya Ine Chauta.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova atayamba kuyankhula kudzera mwa Hoseya, Yehova anati kwa Hoseyayo, “Pita kakwatire mkazi wachiwerewere ndipo ubereke naye ana mʼchiwerewere chake pakuti anthu a mʼdziko muno achimwa pochita chigololo choyipitsitsa, posiya Yehova.” |
koma mwayenda m'njira ya mafumu a Israele, ndi kuchititsa Yuda ndi okhala mu Yerusalemu chigololo, monga umo anachitira chigololo a nyumba ya Ahabu, mwaphanso abale anu a nyumba ya atate wanu, ndiwo abwino akuposa inu;
Pakuti, taonani, iwo okhala patali ndi Inu adzaonongeka; muononga onse akupembedza kwina, kosiyana ndi Inu.
Pakuti anthu anga anachita zoipa ziwiri; anandisiya Ine kasupe wa madzi amoyo, nadziboolera zitsime, zitsime zong'aluka, zosakhalamo madzi.
Pakuti kale lomwe ndinathyola goli lako, ndi kudula zomangira zako; ndipo unati, Sindidzakutumikirani, pakuti pa zitunda zonse zazitali, ndi patsinde pa mitengo yonse yaiwisi unawerama, ndi kuchita dama.
Bwanji uti, Sindinaipitsidwe, sindinatsate Abaala? Ona njira yako m'chigwa, dziwa chimene wachichita; ndiwe ngamira yothamanga yoyenda m'njira zake;
Ndipo kunali kuti mbiri ya dama lake inaipitsa dziko, ndipo anachita chigololo ndi miyala ndi mitengo.
Pamenepo akupulumuka anu adzandikumbukira Ine kwa amitundu kumene anatengedwa ndende, kuti ndasweka ndi mtima wao wachigololo wolekana ndi Ine, ndi maso ao achigololo akutsata mafano ao; ndipo iwo adzakhala onyansa pamaso pao pa iwo eni, chifukwa cha zoipa anazichita m'zonyansa zao zonse.
Ndipo adzatsata omkonda koma osawagwira, adzawafunafuna koma osawapeza; pamenepo adzati, Ndidzamuka ndi kubwererana ndi mwamuna wanga woyamba, popeza pamenepo panandikomera koposa tsopano.
Ndipo Yehova anati kwa ine, Mukanso, konda mkazi wokondedwa ndi bwenzi lake, koma wakuchita chigololo, monga Yehova akonda ana a Israele, angakhale atembenukira kumilungu ina, nakonda nchinchi za mphesa zouma.
Ndimdziwa Efuremu, ndi Israele sandibisikira; pakuti Efuremu iwe, wachita uhule tsopano, Israele wadetsedwa.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, udzagona tulo ndi makolo ako; ndi anthu awa adzauka, nadzatsata ndi chigololo milungu yachilendo ya dziko limene analowa pakati pake, nadzanditaya Ine, ndi kuthyola chipangano changa ndinapangana naocho.
okhala nao maso odzala ndi chigololo, osakhoza kuleka uchimo, kunyengerera iwo a moyo wosakhazikika; okhala nao mtima wozolowera kusirira; ana a temberero;
ndipo pamphumi pake padalembedwa dzina, CHINSINSI, BABILONI WAUKULU, AMAI WA ACHIGOLOLO NDI WA ZONYANSITSA ZA DZIKO.