Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Hoseya 5:3 - Buku Lopatulika

3 Ndimdziwa Efuremu, ndi Israele sandibisikira; pakuti Efuremu iwe, wachita uhule tsopano, Israele wadetsedwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndimdzaiwa Efuremu, ndi Israele sandibisikira; pakuti Efuremu iwe, wachita uhule tsopano, Israele wadetsedwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 “Aefuremu ndikuŵadziŵa, Aisraele ndi osabisika kwa Ine. Aefuremu akhala osakhulupirika, Aisraele adziipitsa.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Ndimadziwa zonse za Efereimu; Aisraeli ndi osabisika kwa Ine. Efereimu wayamba tsopano kuchita zachiwerewere; Israeli wadziyipitsa.

Onani mutuwo Koperani




Hoseya 5:3
24 Mawu Ofanana  

Popeza kuti asanadziwe mwanayo kukana choipa ndi kusankha chabwino, dziko limene mafumu ake awiri udana nao lidzasiyidwa.


Yehova adzatengera pa iwe, ndi pa anthu ako, ndi pa nyumba ya atate wako, masiku, akuti sanadze oterewa kuyambira tsiku limene Efuremu analekana ndi Yuda; kunena mfumu ya Asiriya.


Chifukwa Aramu ndi Efuremu, ndi mwana wa Remaliya anapangana kukuchitira zoipa, nati,


Chiyambi cha kunena kwa Yehova mwa Hoseya. Ndipo Yehova anati kwa Hoseya, Muka, udzitengere mkazi wachigololo ndi ana achigololo; pakuti dziko latsata chigololo chokhachokha kuleka kutsata Yehova.


Efuremu akudya mphepo, natsata mphepo ya kum'mawa; tsiku lonse achulukitsa mabodza ndi chipasuko, ndipo achita pangano ndi Asiriya, natenga mafuta kunka nao ku Ejipito.


Pamene Efuremu analankhula panali kunjenjemera; anadzikweza mu Israele; koma pamene anapalamula mwa Baala, anafa.


Ndinakudziwa m'chipululu, m'dziko lotentha kwambiri.


Efuremu azunzika, apsinjika pa mlanduwo; pakuti anafuna mwini wake kutsata lamulolo.


Pamene Efuremu anaona nthenda yake, ndi Yuda bala lake, Efuremu anamuka kwa Asiriya, natumiza kwa mfumu Yarebu; koma iye sakhoza kukuchiritsani, kapena kupoletsa bala lanu.


Efuremu adzasanduka bwinja tsiku lakudzudzula; mwa mafuko a Israele ndadziwitsa chodzachitikadi.


M'nyumba ya Israele ndinaona chinthu choopsetsa; pamenepo pali uhule wa Efuremu; Israele wadetsedwa.


Efuremu iwe, ndidzakuchitira chiyani? Yuda iwe, ndikuchitire chiyani? Pakuti kukoma mtima kwako kukunga mtambo wam'mawa ndi ngati mame akuphawa mamawa.


Popeza Efuremu anachulukitsa maguwa a nsembe akuchimwako, maguwa a nsembe omwewo anamchimwitsa.


Inu nokha ndinakudziwani mwa mabanja onse a padziko lapansi, m'mwemo ndidzakulangani chifukwa cha mphulupulu zanu zonse.


Pakuti ndidziwa kuti zolakwa zanu nzochuluka, ndi machimo anu ndi olimba, inu akusautsa olungama, akulandira chokometsera mlandu, akukankha osowa kuchipata.


Woyamba kubadwa wa ng'ombe yake, ulemerero ndi wake; nyanga zake ndizo nyanga zanjati; adzatunga nazo mitundu ya anthu pamodzi, kufikira malekezero a dziko lapansi. Iwo ndiwo zikwi khumi za Efuremu, iwo ndiwo zikwi za Manase.


Ndipo palibe cholembedwa chosaonekera pamaso pake, koma zonse zikhala za pambalambanda ndi zovundukuka pamaso pake pa Iye amene tichita naye.


Ndidziwa ntchito zako, kuti suli wozizira kapena wotentha: mwenzi utakhala wozizira kapena wotentha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa