Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 2:20 - Buku Lopatulika

20 Pakuti kale lomwe ndinathyola goli lako, ndi kudula zomangira zako; ndipo unati, Sindidzakutumikirani, pakuti pa zitunda zonse zazitali, ndi patsinde pa mitengo yonse yaiwisi unawerama, ndi kuchita dama.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Pakuti kale lomwe ndinathyola goli lako, ndi kudula zomangira zako; ndipo unati, Sindidzakutumikirani, pakuti pa zitunda zonse zazitali, ndi patsinde pa mitengo yonse yaiwisi unawerama, ndi kuchita dama.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 “Kuyambira masiku amakedzana inu mudathyola goli lanu ndi kudula nsinga zanu. Mudati, ‘Sitidzakutumikirani!’ Ndithu inu mwakhala ngati mkazi wadama, mukupembedza milungu ina pochita zadama pa phiri lililonse ndiponso pansi pa mtengo wogudira uliwonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 “Kuyambira kalekale inu munathyola goli lanu ndi kudula msinga zanu; munanena kuti, ‘Sitidzakutumikirani!’ Ndithudi, inu mwakhala ngati mkazi wachiwerewere. Mukupembedza milungu ina pa phiri lililonse lalitali ndiponso pansi pa mtengo uliwonse wa masamba ambiri.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 2:20
50 Mawu Ofanana  

Ndipo Yerobowamu anaika madyerero mwezi wachisanu ndi chitatu, tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi olingana ndi madyerero aja a ku Yuda, napereka nsembe paguwa la nsembe; anatero mu Betele, nawaphera nsembe anaang'ombe aja anawapanga, naika mu Betele ansembe a misanje imene anaimanga.


Pakuti anadzimangiranso misanje, ndi zoimiritsa, ndi zifanizo, pa chitunda chonse chachitali, ndi patsinde pa mtengo wogudira uliwonse;


Anawatulutsa mumdima ndi mu mthunzi wa imfa, nadula zomangira zao.


Tidule zomangira zao, titaye nsinga zao.


Ndipo anautsa mtima wake ndi malo amsanje ao, namchititsa nsanje ndi mafano osema.


Ndipo anthu onse anavomera pamodzi, nati, Zonse adazilankhula Yehova tidzazichita. Ndipo Mose anabwera nao mau a anthu kwa Yehova.


Ndipo Mose anadza nafotokozera anthu mau onse a Yehova, ndi maweruzo onse; ndipo anthu onse anavomera pamodzi, nati, Mau onse walankhula Yehova tidzachita.


ndipo ndatsikira kuwalanditsa m'manja a anthu a Ejipito, ndi kuwatulutsa m'dziko lija akwere nalowe m'dziko labwino ndi lalikulu, m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; ku malo a Akanani, ndi Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi.


Mzinda wokhulupirika wasanduka wadama! Wodzala chiweruzowo! Chilungamo chinakhalamo koma tsopano ambanda.


Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti katundu wake adzachoka pa phewa lako, ndi goli lake pakhosi pako; ndipo goli lidzathedwa chifukwa cha kudzoza mafuta.


kuti Ine ndidzathyola Aasiriya m'dziko langa, ndi pamwamba pa mapiri anga ndidzawapondereza; pomwepo goli lake lidzachoka pa iwo, ndi katundu wake adzachoka paphewa pao.


Pakuti goli la katundu wake, ndi mkunkhu wa paphewa pake, ndodo ya womsautsa, inu mwazithyola monga tsiku la Midiyani.


Ndaona zonyansa zako, ndi zigololo zako, ndi zakumemesa zako, ndi chinyerinyeri cha dama lako, pamapiri ndi m'munda. Tsoka kwa iwe, Yerusalemu! Sudzayeretsedwa; kodi zidzatero mpaka liti?


Pokumbukira ana ao maguwa a nsembe ao ndi zoimiritsa zao kumitengo yaiwisi ya pa zitunda zazitali.


Mbadwo inu, taonani mau a Yehova. Kodi ndakhala kwa Israele chipululu? Kapena dziko la mdima woti bii? Chifukwa ninji ati anthu anga, Tamasuka sitidzabweranso konse kwa Inu?


Koma vomereza zoipa zako, kuti walakwira Yehova Mulungu wako, ndi kupatukira mwa alendo patsinde pa mitengo yaiwisi yonse, ndipo sunamvere mau anga, ati Yehova.


Pakuti padzakhala tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, kuti ndidzathyola goli lake pakhosi pako, ndipo ndidzadula zomangira zako; ndipo alendo sadzamuyesanso iye mtumiki wao;


Ine ndidzanka kwa akulu, ndidzanena ndi iwo; pakuti adziwa njira ya Yehova, ndi chiweruzo cha Mulungu wao. Koma awa anavomerezana nathyola goli, nadula zomangira zao.


Unachitanso chigololo ndi Aasiriya, pakuti unakhala wosakoledwa, inde unachita chigololo nao, koma sunakoledwe.


Pakumanga nyumba yako yachimphuli pa mphambano zilizonse, ndi pomanga chiunda chako m'makwalala ali onse, sunakhale ngati mkazi wadama waphindu, popeza unapeputsa mphotho.


Ndipo adzatentha nyumba zako ndi moto, nadzakuweruza pamaso pa akazi ambiri; ndipo ndidzakuleketsa kuchita chigololo, ndipo sudzalipiranso mphotho yachigololo.


Nditafika nao m'dzikolo ndinawakwezera dzanja langa kuwapatsa ilo, anapenya chitunda chilichonse chachitali, ndi mtengo uliwonse wagudugudu, naphera pomwepo nsembe zao, naperekapo nsembe zao zondiputa, aponso anachita fungo lao lokoma, nathiraponso nsembe zao zothira.


Koma Ohola anachita chigololo pamene anali wanga, anaumirira mabwenzi ake Aasiriya oyandikizana naye;


Chiyambi cha kunena kwa Yehova mwa Hoseya. Ndipo Yehova anati kwa Hoseya, Muka, udzitengere mkazi wachigololo ndi ana achigololo; pakuti dziko latsata chigololo chokhachokha kuleka kutsata Yehova.


Pakuti mai wao anachita chigololo; iye amene anali ndi pakati pa iwo anachita chamanyazi; pakuti anati, Ndidzatsata ondikondawo, akundipatsa ine chakudya changa, ndi madzi anga, ubweya wanga, ndi thonje langa, mafuta anga, ndi chakumwa changa.


ndipo ndinati kwa iye, Uzikhala ndi ine masiku ambiri, usachita chigololo, usakhala mkazi wa mwamuna aliyense; momwemo inenso nawe.


Pamwamba pa mapiri aphera nsembe, nafukiza pazitunda, patsinde pa thundu, ndi minjali, ndi mkundi; popeza mthunzi wake ndi wabwino, chifukwa chake ana anu aakazi achita uhule, ndi apongozi anu achita chigololo.


Usakondwera, Israele, ndi kusekerera, ngati mitundu ya anthu; pakuti wachita chigololo kuleka Mulungu wako, wakonda mphotho ya chigololo pa dwale la tirigu lililonse.


Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani m'dziko la Ejipito, kuti musakhale akapolo ao; ndipo ndinathyola mitengo ya magoli anu, ndi kukuyendetsani choweramuka.


Koma tsopano ndidzathyola ndi kukuchotsera goli lake, ndipo ndidzadula zomangira zako.


Muononge konse malo onse, amitundu amene mudzawalanda anatumikirako milungu yao, pa mapiri aatali, ndi pa zitunda, ndi pansi pa mitengo yonse yabiriwiri;


Ndipo mukumbukire kuti munali akapolo m'dziko la Ejipito, ndipo Yehova Mulungu wanu anakuombolani; chifukwa chake ndikuuzani ichi lero lino.


Mwalonjezetsa Yehova lero kuti adzakhala Mulungu wanu, ndi kuti mudzayenda m'njira zake, ndi kusunga malemba ake, ndi malamulo ake, ndi maweruzo ake, ndi kumvera mau ake.


Koma Yehova anakutengani, nakutulutsani m'ng'anjo yamoto, mu Ejipito, mukhale kwa Iye anthu a cholowa chake, monga mukhala lero lino.


Kapena kodi anayesa Mulungu kumuka ndi kudzitengera mtundu mwa mtundu wina wa anthu, ndi mayesero, ndi zizindikiro, ndi zozizwa, ndi nkhondo, ndi mwa dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi mwa zoopsa zazikulu, monga mwa zonse Yehova Mulungu wanu anakuchitirani mu Ejipito pamaso panu?


Yandikizani inu, ndi kumva zonse Yehova Mulungu wathu adzati; ndipo inu munene ndi ife zonse zimene Yehova Mulungu wathu adzanena ndi inu; ndipo ife tidzazimva ndi kuzichita.


Ndipo anamyankha Yoswa, nati, Zonse mwatilamulira tidzachita, ndipo kulikonse mutitumako tidzamuka.


Ndipo anthu anati kwa Yoswa, Tidzamtumikira Yehova Mulungu wathu ndi kumvera mau ake.


Ndipo Yoswa analembera mau awa m'buku la chilamulo cha Mulungu; natenga mwala waukulu, nauimitsa apo patsinde pa thundu wokhala pamalo opatulika a Yehova.


Ndipo anadza mmodzi mwa angelo asanu ndi awiri akukhala nazo mbale zisanu ndi ziwiri, nalankhula ndi ine, nanena, Idza kuno, ndidzakuonetsa chitsutso cha mkazi wachigololo wamkulu, wakukhala pamadzi ambiri,


Ndipo ana a Israele anaonjeza kuchita choipa pamaso pa Yehova, natumikira Abaala, ndi Aasitaroti, ndi milungu ya Aramu, ndi milungu ya Sidoni, ndi milungu ya Mowabu, ndi milungu ya ana a Amoni, ndi milungu ya Afilisti; ndipo anamleka Yehova osamtumikira.


Ndipo ana a Israele anachita choipa pamaso pa Yehova, natumikira Abaala;


Ndipo anasiya Yehova, natumikira Baala ndi Asitaroti.


Ndipo anapemphera kwa Yehova, kuti, Tinachimwa, popeza tinasiya Yehova, ndi kutumikira Abaala ndi Asitaroti, koma mutipulumutse tsopano m'manja a adani anthu, ndipo tidzakutumikirani Inu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa