Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 2:23 - Buku Lopatulika

23 Bwanji uti, Sindinaipitsidwe, sindinatsate Abaala? Ona njira yako m'chigwa, dziwa chimene wachichita; ndiwe ngamira yothamanga yoyenda m'njira zake;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Bwanji uti, Sindinaipitsidwa, sindinatsata Abaala? Ona njira yako m'chigwa, dziwa chimene wachichita; ndiwe ngamira yothamanga yoyenda m'njira zake;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 “Uneneranji kuti, ‘Ine sindidadziipitse, sindidatsate Baala?’ Kumbukira m'mene udachimwira m'chigwamo, zindikira zimene wachita. Wakhala ngati ngamira yaikazi, yothamanga uku ndi uku.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 “Iwe ukunena bwanji kuti, ‘Ine sindinadziyipitse; sindinatsatire Abaala’? Takumbukira mmene unkandichimwira mʼchigwa muja; zindikira bwino zomwe wachita. Iwe uli ngati ngamira yayikazi yaliwiro yomangothamanga uku ndi uku,

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 2:23
24 Mawu Ofanana  

Ayuda anali nako kuunika, ndi kukondwera, ndi chimwemwe, ndi ulemu.


Pakuti adzidyoletsa yekha m'kuona kwake, kuti anthu sadzachipeza choipa chake ndi kukwiya nacho.


Izi unazichita iwe, ndipo ndinakhala chete Ine; unayesa kuti ndifanana nawe, ndidzakudzudzula, ndi kuchilongosola pamaso pako.


Wobisa machimo ake sadzaona mwai; koma wakuwavomereza, nawasiya adzachitidwa chifundo.


Pali mbadwo wodziyesa oyera, koma osasamba litsiro lao.


Chomwecho njira ya mkazi wachigololo; adya, napukuta pakamwa, nati, Sindinachite zoipa.


Atero Yehova kwa anthu awa, Chomwecho akonda kusocherera; sanakanize mapazi ao; chifukwa chake Yehova sawalandira; tsopano adzakumbukira choipa chao, nadzalanga zochimwa zao.


Ndipo padzakhala, pamene udzaonetsa anthu awa mau awa onse, ndipo iwo adzati kwa iwe, Chifukwa chake nchiyani kuti Yehova watinenera ife choipa chachikulu ichi? Mphulupulu yathu ndi yanji? Tchimo lathu lanji limene tachimwira Yehova Mulungu wathu?


Bwanji uyendayenda kwambiri ndi kusintha njira yako? Udzachitanso manyazi ndi Ejipito monga unachita manyazi ndi Asiriya.


Kwezera maso ako kumapiri oti see, nuone: sanagone ndi iwe kuti? Panjira wakhalira iwo, monga Mwarabu m'chipululu; ndipo waipitsa dziko ndi zigololo zako, ndi zoipa zako.


Udzayenda kwina ndi kwina masiku angati, iwe mwana wamkazi wobwerera m'mbuyo? Pakuti Yehova walenga chatsopano m'dziko lapansi: mkazi adzasanduka mphongo.


Namanga akachisi a ku Tofeti, kuli m'chigwa cha mwana wa Hinomu, kuti atenthe m'moto ana ao aamuna ndi aakazi; chimene sindiwanauze iwo, sichinalowe m'mtima mwanga.


koma anatsata kuuma kwa mtima wao, ndi Baala, monga makolo ao anawaphunzitsa;


Chiyambi cha kunena kwa Yehova mwa Hoseya. Ndipo Yehova anati kwa Hoseya, Muka, udzitengere mkazi wachigololo ndi ana achigololo; pakuti dziko latsata chigololo chokhachokha kuleka kutsata Yehova.


Koma iye, pofuna kudziyesa yekha wolungama, anati kwa Yesu, Ndipo mnansi wanga ndani?


Ndipo tidziwa kuti zinthu zilizonse chizinena chilamulo chizilankhulira iwo ali nacho chilamulo; kuti pakamwa ponse patsekedwe, ndi dziko lonse lapansi litsutsidwe ndi Mulungu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa