ndipo ndidzakulumbiritsa iwe pa Yehova, Mulungu wa Kumwamba, ndi Mulungu wa dziko lapansi, kuti usadzamtengere mwana wanga mkazi wa kwa ana aakazi a Akananiwo, amene ndikhala pakati pao.
Genesis 28:1 - Buku Lopatulika Ndipo Isaki anamuitana Yakobo, namdalitsa iye, namuuza iye, nati kwa iye, Usatenge mkazi wa ana aakazi a Kanani. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Isaki anamuitana Yakobo, namdalitsa iye, namuuza iye, nati kwa iye, Usatenge mkazi wa ana akazi a Kanani. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo Isaki adaitana Yakobe namdalitsa, ndipo adamlamula kuti, “Usakwatire mkazi wa kuno ku Kanani. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho Isake anayitanitsa Yakobo namudalitsa nʼkumuwuzitsa kuti, “Usakwatire mkazi wa kuno ku Kanaani. |
ndipo ndidzakulumbiritsa iwe pa Yehova, Mulungu wa Kumwamba, ndi Mulungu wa dziko lapansi, kuti usadzamtengere mwana wanga mkazi wa kwa ana aakazi a Akananiwo, amene ndikhala pakati pao.
Ndipo mbuyanga anandilumbiritsa ine kuti, Usamtengere mwana wanga mkazi wa ana aakazi a Kanani, m'dziko mwao m'mene ndikhala ine;
nundikonzere ine chakudya chokolera chonga chomwe ndichikonda ine, nudze nacho kwa ine kuti ndidzadye; kuti moyo wanga ukadalitse iwe ndisanafe.
Ndipo anati Rebeka kwa Isaki, Ndalema moyo wanga chifukwa cha ana aakazi a Ahiti, akatenga Yakobo mkazi wa ana aakazi a Ahiti, onga ana aakazi a m'dziko lino, moyo wanga udzandikhalira ine bwanji?
Ndipo anaona Esau kuti Isaki anamdalitsa Yakobo namtumiza ku Padanaramu kuti atenge mkazi wa kumeneko; ndiponso kuti pamene anamdalitsa iye, anamuuza iye kuti, Usatenge mkazi wa ana aakazi a Kanani;
pamenepo tidzakupatsani inu ana athu aakazi, ndipo tidzadzitengera ana anu aakazi, ndipo tidzakhala pamodzi ndi inu, ndi kukhala mtundu umodzi.
Mukwatirane ndi ife: tipatseni ife ana anu akazi, ndiponso dzitengereni ana athu aakazi.
Ndipo Yuda anaona kumeneko mwana wamkazi wa Mkanani dzina lake Suwa: ndipo anamtenga, nalowa kwa iye.
Ndipo anadalitsa Yosefe, nati, Mulungu, pamaso pake anayenda makolo anga Abrahamu ndi Isaki, Mulungu amene anandidyetsa ine nthawi zonse za moyo wanga kufikira lero,
Awa onse ndiwo mafuko khumi ndi awiri a Israele: izo ndizo zomwe ananena kwa iwo atate wao nawadalitsa; yense monga mdalitso wake anawadalitsa.
kuti ana aamuna a Mulungu anayang'ana ana aakazi a anthu, kuti iwo anali okongola; ndipo anadzitengera okha akazi onse amene anawasankha.
tengani akazi, balani ana aamuna ndi aakazi; kwatitsani ana anu aamuna, patsani ananu aakazi kwa amuna, kuti abale ana aamuna ndi aakazi; kuti mubalane pamenepo musachepe.
Ndipo gawo limodzi la fuko la Manase, Mose anawapatsa cholowa mu Basani; koma gawo lina Yoswa anawaninkha cholowa pakati pa abale ao tsidya lija la Yordani kumadzulo. Ndiponso pamene Yoswa anawauza amuke ku mahema ao, anawadalitsa;