Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 49:28 - Buku Lopatulika

28 Awa onse ndiwo mafuko khumi ndi awiri a Israele: izo ndizo zomwe ananena kwa iwo atate wao nawadalitsa; yense monga mdalitso wake anawadalitsa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

28 Awa onse ndiwo mafuko khumi ndi awiri a Israele: izo ndizo zomwe ananena kwa iwo atate wao nawadalitsa; yense monga mdalitso wake anawadalitsa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

28 Aŵa ndiwo akulu a mafuko khumi ndi aŵiri a Aisraele, ndipo zimenezi nzimene bambo wao Yakobe adaŵauza, pamene ankadalitsa aliyense mwa iwo potsazikana nawo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

28 Onse awa ndi mafuko khumi ndi awiri a Israeli, ndipo zimenezi ndi zomwe abambo awo ananena pamene anawadalitsa, kuwapatsa aliyense madalitso ake womuyenera iye.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 49:28
16 Mawu Ofanana  

Ndipo panali pamene Israele anakhala m'dzikomo, Rubeni anamuka nagona ndi Biliha, mkazi wamng'ono wa atate wake: ndipo Israele anamva. Ana aamuna a Yakobo anali khumi ndi awiri:


Benjamini ndiye mmbulu wakulusalusa; m'mamawa adzadya chomotola, madzulo adzagawa zofunkha.


Ndipo analangiza iwo nati kwa iwo, Ine nditi ndisonkhanitsidwe kwa anthu a mtundu wanga; mundiike ine pamodzi ndi makolo anga m'phanga lili m'munda wa Efuroni Muhiti,


Ndipo Eliya anatenga miyala khumi ndi iwiri, monga mwa ziwerengo cha mafuko ana a Yakobo, amene mau a Yehova adamfikira, kuti, Dzina lako ndi Israele.


m'menemo mfumu inalola Ayuda okhala mu mzinda uliwonse asonkhane, ndi kulimbikira moyo wao, kuononga, kupha, ndi kupulula mphamvu yonse ya anthu ndi ya dziko yofuna kuwathira nkhondo, iwo, ana ao aang'ono, ndi akazi ao, ndi kulanda zofunkha zao,


Pamenepo mfumu Ahasuwero anati kwa mkazi wamkulu Estere, ndi kwa Mordekai Myuda, Taonani, ndampatsa Estere nyumba ya Hamani, ndi iyeyu anampachika pamtanda, chifukwa anatulutsa dzanja lake pa Ayuda.


Pamenepo anaitana alembi a mfumu nthawi yomweyo, mwezi wachitatu, ndiwo mwezi wa Sivani, tsiku lake la makumi awiri ndi chitatu, monga mwa zonse Mordekai analamulira; nalembera kwa Ayuda, ndi kwa akazembe, ndi ziwanga, ndi akalonga a kumaiko, oyambira ku Indiya, ofikira ku Kusi, maiko zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi awiri, ku dziko lililonse monga mwa chilembedwe chao, ndi mtundu uliwonse monga mwa chinenedwe chao, ndi kwa Ayuda monga mwa chinenedwe chao.


Ndi miyalayi ikhale monga mwa maina a ana a Israele, khumi ndi awiri, monga maina ao; monga malochedwe a chosindikizira, yonse ikhale monga maina ao, kwa mafuko khumi ndi awiri.


Taonani, anthuwo auka ngati mkango waukazi, nadzitukumula ngati mkango waumuna. Sugonanso kufikira utadya nyama yogwira, utamwa mwazi wa zophedwa.


kufikira komweko mafuko athu khumi ndi awiri, potumikira Mulungu kosapumula usiku ndi usana, ayembekeza kufikirako. Chifukwa cha chiyembekezo ichi, Mfumu, andinenera Ayuda.


Ndipo mdalitso, Mose munthu wa Mulungu anadalitsa nao ana a Israele asanafe, ndi uwu.


Yakobo, kapolo wa Mulungu ndi wa Ambuye Yesu Khristu, kwa mafuko khumi ndi awiri a m'chibalaliko: ndikupatsani moni.


Ndipo ndinamva chiwerengo cha iwo osindikizidwa chizindikiro, zikwi makumi khumi ndi makumi anai mphambu anai, osindikizidwa chizindikiro mwa mafuko onse a ana a Israele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa