Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 27:46 - Buku Lopatulika

46 Ndipo anati Rebeka kwa Isaki, Ndalema moyo wanga chifukwa cha ana aakazi a Ahiti, akatenga Yakobo mkazi wa ana aakazi a Ahiti, onga ana aakazi a m'dziko lino, moyo wanga udzandikhalira ine bwanji?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

46 Ndipo anati Rebeka kwa Isaki, Ndalema moyo wanga chifukwa cha ana akazi a Heti: akatenga Yakobo mkazi wa ana akazi a Heti, onga ana akazi a m'dziko lino, moyo wanga udzandikhalira ine bwanji?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

46 Rebeka adauza Isaki kuti, “Akazi Achihitiŵa, ine ndatopa nawo! Yakobenso akakwatira wina mwa a Ahiti akunoŵa, ine kodi moyo wanga nkukomanso?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

46 Tsono Rebeka anati kwa Isake, “Ine sindikukondwera nawo anamwali a Chihiti. Ndipo ngati Yakobo angapeze mbeta kuno mwa anamwali a Chihitiwa, ndiye kuli bwino kungofa.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 27:46
11 Mawu Ofanana  

ndipo ndidzakulumbiritsa iwe pa Yehova, Mulungu wa Kumwamba, ndi Mulungu wa dziko lapansi, kuti usadzamtengere mwana wanga mkazi wa kwa ana aakazi a Akananiwo, amene ndikhala pakati pao.


ndipo Esau anaona kuti ana aakazi a Kanani sanakondweretse Isaki atate wake:


Koma iye mwini analowa m'chipululu ulendo wa tsiku limodzi, nakakhala pansi patsinde pa mtengo watsanya, napempha kuti afe; nati, Kwafikira, chotsani tsopano moyo wanga, Yehova; popeza sindili wokoma woposa makolo anga.


Ha? Mukadandibisa kumanda, mukadandisunga m'tseri, mpaka wapita mkwiyo wanu. Mukadandiikira nthawi, ndi kundikumbukira.


Ndinyansidwa nao moyo wanga; sindidzakhala ndi moyo chikhalire; mundileke; pakuti masiku anga ndi achabe.


Ndipo tsopano, Yehova, mundichotseretu moyo wanga, kundikomera ine kufa, osakhala ndi moyo ai.


Ndipo Mulungu anati kwa Yona, Uyenera kodi kupsa mtima chifukwa cha msatsiwo? Nati iye, Ee, kundiyenera ine kupsa mtima mpaka imfa.


Ndipo ngati mundichitira chotero, mundiphetu tsopano apa, ngati ndapeza ufulu pamaso panu, ndisayang'ane tsoka langa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa