Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 27:45 - Buku Lopatulika

45 mpaka utamchokera mkwiyo mkulu wako, kuti aiwale chimene wamchitira iye; pamenepo ndipo ndidzatumiza kukutenganso iwe kumeneko; ndidzakhala bwanji wopanda inu nonse awiri tsiku limodzi?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

45 mpaka wakuchokera mkwiyo wa mkulu wako, kuti aiwale chimene wamchitira iye; pamenepo ndipo ndidzatumiza kukutenganso iwe kumeneko; ndidzakhala bwanji wopanda inu nonse awiri tsiku limodzi?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

45 mpaka mtima wa mbale wako utatsika ndi kuiŵala zonse zimene wamchitazi. Pa nthaŵiyo, ine ndidzatuma munthu kudzakutenga. Nanga nditayirenji inu ana anga aŵiri pa tsiku limodzi?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

45 Tsono mkwiyo wa mʼbale wakoyo ukadzatsika ndi kuyiwala zonse wamuchitirazi, ndidzatuma munthu kuti adzakutenge. Nanga nditayirenji nonse awiri nthawi imodzi?”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 27:45
10 Mawu Ofanana  

Kapena atate wanga adzandiyambasa, ndipo ndidzaoneka pamaso pake ngati wakunyenga; pamenepo ndidzadzitengera ine temberero, si mdalitso.


Ndipo Yakobo anati kwa atate wake, Ndine Esau mwana wanu wamkulu; ndachita monga mwandiuza ine; ukanitu, khalani tsonga, idyani nyama yanga kuti moyo wanu undidalitse ine.


Ndipo iye anati, Mphwako anadza monyenga, nalanda mdalitso wako.


Muli zolingalira zambiri m'mtima mwa munthu; koma uphungu wa Yehova ndiwo udzaimika.


Ndani anganene, chonena chake ndi kuchitikadi, ngati Ambuye salamulira?


Koma pamene akunjawo anaona chilombocho chili lende padzanja lake, ananena wina ndi mnzake, Zoona munthuyu ndiye wambanda. Angakhale anapulumuka m'nyanja, chilungamo sichimlola akhale ndi moyo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa