Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa namanga bulu wake, natengako anyamata ake awiri pamodzi naye, ndi Isaki mwana wake, nawaza nkhuni za nsembe yopsereza, nauka, nanka kumalo komwe Mulungu anamuuza iye.
Genesis 22:4 - Buku Lopatulika Tsiku lachitatu Abrahamu anatukula maso ake naona malowo patali. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tsiku lachitatu Abrahamu anatukula maso ake naona malowo patali. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pa tsiku lachitatu lake Abrahamu adaona malowo chapatali. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pa tsiku lachitatu, Abrahamu anakweza maso ake ndipo anaona malowo chapatali. |
Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa namanga bulu wake, natengako anyamata ake awiri pamodzi naye, ndi Isaki mwana wake, nawaza nkhuni za nsembe yopsereza, nauka, nanka kumalo komwe Mulungu anamuuza iye.
Ndipo Abrahamu anati kwa anyamata ake, Khalani kuno ndi bulu, ine ndi mwanayu tinka uko, ndipo tikapemphera ndi kubweranso kwa inu.
Bwerera, nunene kwa Hezekiya mtsogoleri wa anthu anga, Atero Yehova Mulungu wa Davide kholo lako, Ndamva pemphero lako, ndapenya misozi yako; taona, ndidzakuchiritsa, tsiku lachitatu udzakwera kunka kunyumba ya Yehova.
Ndipo kunali tsiku lachitatu, Estere anavala zovala zake zachifumu, nakaimirira m'bwalo la m'kati la nyumba ya mfumu, popenyana pa nyumba ya mfumu; ndi mfumu inakhala pa mpando wake wachifumu m'nyumba yachifumu, pandunji polowera m'nyumba.
Ndipo Mose anatsogolera Israele kuchokera ku Nyanja Yofiira, ndipo anatulukako nalowa m'chipululu cha Suri; nayenda m'chipululu masiku atatu, osapeza madzi.
Nakonzekeretu tsiku lachitatu; pakuti tsiku lachitatu Yehova adzatsika paphiri la Sinai pamaso pa anthu onse.
Ndipo iwo anati, Mulungu wa Ahebri wakomana ndi ife; timuketu ulendo wa masiku atatu m'chipululu, kumphera nsembe Yehova Mulungu wathu; kuti angatikanthe ndi mliri, kapena ndi lupanga.
Atapita masiku awiri adzatitsitsimutsa, tsiku lachitatu adzatiutsa; ndipo tidzakhala ndi moyo pamaso pake.
Ndipo anayenda kuchokera kuphiri la Yehova ulendo wa masiku atatu; ndipo likasa la chipangano cha Yehova, linawatsogolera ulendo wa masiku atatu kuwafunira popumulira.
iyeyo adziyeretse nao tsiku lachitatu, ndi pa tsiku lachisanu ndi chiwiri adzakhala woyera; koma akapanda kudziyeretsa tsiku lachitatu, sadzakhala woyera tsiku lachisanu ndi chiwiri.
Ndipo woyerayo awaze pa wodetsedwayo tsiku lachitatu, ndi tsiku lachisanu ndi chiwiri; ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri amyeretse; ndipo atsuke zovala zake, nasambe m'madzi, nadzakhala woyera madzulo.
Ndipo mukhale m'misasa kunja kwa chigono masiku asanu ndi awiri; aliyense adapha munthu, ndi aliyense wakukhudza wophedwa, mudziyeretse tsiku lachitatu ndi lachisanu ndi chiwiri, inu ndi andende anu.
ndipo adzamupha Iye, ndipo Iye adzauka tsiku lachitatu. Ndipo iwo anali ndi chisoni chachikulu.
Ndipo Iye anati kwa iwo, Pitani kauzeni nkhandweyo, Taonani, nditulutsa ziwanda, nditsiriza machiritso lero ndi mawa, ndipo mkucha nditsirizidwa.
Pitani pakati pa chigono, nimulamulire anthu, ndi kuti, Mudzikonzeretu kamba, pakuti asanapite masiku atatu mudzaoloka Yordani uyu, kulowa ndi kulandira dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, likhale lanulanu.
Ndipo Davide anaolokera kutsidya, naima patali pamwamba paphiri; pakati pao panali danga lalikulu;