Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 1:11 - Buku Lopatulika

11 Pitani pakati pa chigono, nimulamulire anthu, ndi kuti, Mudzikonzeretu kamba, pakuti asanapite masiku atatu mudzaoloka Yordani uyu, kulowa ndi kulandira dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, likhale lanulanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Pitani pakati pa chigono, nimulamulire anthu, ndi kuti, Mudzikonzeretu kamba, pakuti asanapite masiku atatu mudzaoloka Yordani uyu, kulowa ndi kulandira dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, likhale lanulanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 “Pitani ku zithando zonse, mukauze anthu kuti, ‘Konzekani, mangani katundu, chifukwa atapita masiku atatu, mudzaoloka Yordani ndi kulandira dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsani.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 “Pitani ku misasa yonse ndipo muwuze anthu kuti, ‘Konzekani, mangani katundu wanu, popeza pakapita masiku atatu kuyambira lero mudzawoloka Yorodani kupita kukatenga dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 1:11
9 Mawu Ofanana  

Bwerera, nunene kwa Hezekiya mtsogoleri wa anthu anga, Atero Yehova Mulungu wa Davide kholo lako, Ndamva pemphero lako, ndapenya misozi yako; taona, ndidzakuchiritsa, tsiku lachitatu udzakwera kunka kunyumba ya Yehova.


Nakonzekeretu tsiku lachitatu; pakuti tsiku lachitatu Yehova adzatsika paphiri la Sinai pamaso pa anthu onse.


Atapita masiku awiri adzatitsitsimutsa, tsiku lachitatu adzatiutsa; ndipo tidzakhala ndi moyo pamaso pake.


Pakuti mulinkuoloka Yordani kulowa ndi kulandira dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani; ndipo mudzachilandira cholowa chanu, ndi kukhalamo.


Ndipo ndinauza inu muja, ndi kuti, Yehova Mulungu wanu wakupatsani dziko ili likhale lanulanu, muoloke, amuna onse amphamvu ovala zida zao, pamaso pa abale anu ana a Israele.


Imvani Israele; mulikuoloka Yordani lero lino, kulowa ndi kulandira amitundu akulu ndi amphamvu akuposa inu, mizinda yaikulu ndi ya malinga ofikira kuthambo,


Pamenepo Yoswa analamulira akapitao a anthu, ndi kuti,


Mose mtumiki wanga wafa; tauka tsono, nuoloke Yordani uyu, iwe ndi anthu awa onse, kulowa m'dzikomo ndilikuwapatsa, ndiwo ana a Israele.


Ndipo kunali atapita masiku atatu, akapitao anapita pakati pa chigono;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa