Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 26:13 - Buku Lopatulika

13 Ndipo Davide anaolokera kutsidya, naima patali pamwamba paphiri; pakati pao panali danga lalikulu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndipo Davide anaolokera pa phiri; pakati pao panali danga lalikulu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Pambuyo pake Davide adakwerera mbali ina nakaimirira pamwamba pa phiri, pakati nkusiya mpata waukulu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Pambuyo pake Davide anadutsa nakakwerera mbali ina ya phiri, ndi kuyimirira pamwamba pa phiri patali. Pakati pawo panali mpata waukulu.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 26:13
4 Mawu Ofanana  

Ndipo atamuuza Yotamu, anamuka iye naimirira pamutu paphiri la Gerizimu, nakweza mau ake, nafuula, nanena nao, Mundimvere ine, eni ake a ku Sekemu inu, kuti Mulungu amvere inu.


Bwino lake Davide yemwe ananyamuka, natuluka m'phangamo, nafuulira Saulo, nati, Mbuye wanga, mfumu. Ndipo pakucheuka Saulo, Davide anaweramira nkhope yake pansi, namgwadira.


Chomwecho Davide anatenga mkondowo, ndi chikho cha madzi ku mutu wa Saulo nachoka iwowa, osawaona munthu, kapena kuzidziwa, kapena kugalamuka; pakuti onse anali m'tulo; popeza tulo tatikulu tochokera kwa Yehova tinawagwira onse.


ndipo Davide anaitana anthuwo, ndi Abinere mwana wa Nere, nati Suyankha kodi Abinere? Tsono Abinere anayankha, nati, Ndiwe yani amene uitana mfumuyo?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa