1 Samueli 26:12 - Buku Lopatulika12 Chomwecho Davide anatenga mkondowo, ndi chikho cha madzi ku mutu wa Saulo nachoka iwowa, osawaona munthu, kapena kuzidziwa, kapena kugalamuka; pakuti onse anali m'tulo; popeza tulo tatikulu tochokera kwa Yehova tinawagwira onse. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201412 Chomwecho Davide anatenga mkondowo, ndi chikho cha madzi ku mutu wa Saulo nachoka iwowa, osawaona munthu, kapena kuzidziwa, kapena kugalamuka; pakuti onse anali m'tulo; popeza tulo tatikulu tochokera kwa Yehova tinawagwira onse. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa12 Motero Davide adatenga mkondo ndi mtsuko wa madzi, zimene zinali kumutu kwa Saulo, nachokapo. Palibe amene adaona zimenezo ngakhale kuzidziŵa, ndipo panalibe wina aliyense amene adadzuka. Onse anali m'tulo, chifukwa chakuti Chauta adaaŵagonetsa tulo tofa nato. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero12 Motero Davide anatenga mkondo ndi botolo lamadzi zimene zinali ku mutu kwa Sauli ndipo anachoka. Palibe amene anaona zimenezi kapena kudziwa, ndipo palibenso amene anadzuka. Onse anali mʼtulo, chifukwa Yehova anawagonetsa tulo tofa nato. Onani mutuwo |