Ndipo Mulungu anati, Koma Sara mkazi wako adzakubalira iwe mwana wamwamuna; ndipo udzamutcha dzina lake Isaki; ndipo ndidzalimbikitsa naye pangano langa, kuti likhale pangano la nthawi zonse, la ku mbeu zake za pambuyo pake.
Genesis 21:3 - Buku Lopatulika Ndipo Abrahamu anamutcha dzina lake la mwana wake wamwamuna amene anabala iye, amene anambalira iye Sara, Isaki. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Abrahamu anamutcha dzina lake la mwana wake wamwamuna amene anabala iye, amene anambalira iye Sara, Isaki. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo mwana wa Abrahamuyo, mwana amene Sara adamubalirayo, Abrahamu adamutcha Isaki. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Abrahamu anapereka dzina loti Isake kwa mwana wamwamuna amene Sara anamuberekera. |
Ndipo Mulungu anati, Koma Sara mkazi wako adzakubalira iwe mwana wamwamuna; ndipo udzamutcha dzina lake Isaki; ndipo ndidzalimbikitsa naye pangano langa, kuti likhale pangano la nthawi zonse, la ku mbeu zake za pambuyo pake.
Koma pangano langa ndidzalimbikitsa ndi Isaki, amene Sara adzakubalira iwe nthawi yomwe ino chaka chamawa.
Ndipo Mulungu anati kwa Abrahamu, Usaipidwe nao, chifukwa cha mnyamatayo, ndi chifukwa cha mdzakazi wako; momwe monse akunenera iwe Sara umvere iwe mau ake; chifukwa kuti mwa Isaki zidzaitanidwa mbeu zako.
Ndipo anati, Tengatu mwana wako, wamwamuna wayekhayo, Isaki, amene ukondana naye, numuke ku dziko la Moriya; numpereke iye kumeneko nsembe yopsereza pa limodzi la mapiri lomwe ndidzakuuza iwe.
Abrahamu anabala Isaki; ndi Isaki anabala Yakobo; ndi Yakobo anabala Yuda ndi abale ake;
Ndipo anampatsa iye chipangano cha mdulidwe; ndipo kotero Abrahamu anabala Isaki, namdula tsiku lachisanu ndi chitatu; ndi Isaki anabala Yakobo, ndi Yakobo anabala makolo aakulu aja khumi ndi awiri.
kapena chifukwa ali mbeu ya Abrahamu, siali onse ana; koma anati, Mwa Isaki, mbeu yako idzaitanidwa.
Ndipo ndinamtenga kholo lanu Abrahamu tsidya lija la mtsinje, ndi kumuyendetsa m'dziko lonse la Kanani ndi kuchulukitsa mbeu zake ndi kumpatsa Isaki.