Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 21:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo Sara anatenga pakati, nambalira Abrahamu mu ukalamba wake mwana wamwamuna, nthawi yomweyo Mulungu anamuuza iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo Sara anatenga pakati, nambalira Abrahamu m'ukalamba wake mwana wamwamuna, nthawi yomweyo Mulungu anamuuza iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Choncho Sarayo adatenga pathupi, nabalira Abrahamu mwana wamwamuna pamene Abrahamuyo anali nkhalamba. Mwana ameneyu adabadwa pa nthaŵi yeniyeni imene Mulungu adaanena.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Sara anakhala ndi pathupi ndipo anamuberekera Abrahamu mwana wamwamuna mu ukalamba wake, pa nyengo imene Mulungu anamulonjeza.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 21:2
12 Mawu Ofanana  

Ndipo Mulungu anati, Koma Sara mkazi wako adzakubalira iwe mwana wamwamuna; ndipo udzamutcha dzina lake Isaki; ndipo ndidzalimbikitsa naye pangano langa, kuti likhale pangano la nthawi zonse, la ku mbeu zake za pambuyo pake.


Koma pangano langa ndidzalimbikitsa ndi Isaki, amene Sara adzakubalira iwe nthawi yomwe ino chaka chamawa.


Ndipo anati, Ndidzabwera kwa iwe ndithu pakufika nyengo yake; taonani Sara mkazi wako adzakhala ndi mwana wamwamuna. Ndipo Sara anamva pakhomo pa hema amene anali pambuyo pake.


Kodi chilipo chinthu chomkanika Yehova? Pa nthawi yoikidwa ndidzabwera kwa iwe, pakufika nyengo yake, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.


Ndipo taona, Elizabeti mbale wako, iyenso ali ndi pakati pa mwana wamwamuna mu ukalamba wake; ndipo mwezi uno uli wachisanu ndi chimodzi wa iye amene ananenedwa wouma.


Ndipo anampatsa iye chipangano cha mdulidwe; ndipo kotero Abrahamu anabala Isaki, namdula tsiku lachisanu ndi chitatu; ndi Isaki anabala Yakobo, ndi Yakobo anabala makolo aakulu aja khumi ndi awiri.


Pakuti mau a lonjezo ndi amenewa, Pa nyengo iyi ndidzadza, ndipo Sara adzakhala ndi mwana.


Pakuti palembedwa, kuti Abrahamu anali nao ana aamuna awiri, mmodzi wobadwa mwa mdzakazi, ndi mmodzi wobadwa mwa mfulu.


Ndi chikhulupiriro Sara yemwe analandira mphamvu yakukhala ndi pakati, patapita nthawi yake, popeza anamwerengera wokhulupirika Iye amene adalonjeza;


Ndipo ndinamtenga kholo lanu Abrahamu tsidya lija la mtsinje, ndi kumuyendetsa m'dziko lonse la Kanani ndi kuchulukitsa mbeu zake ndi kumpatsa Isaki.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa