Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 7:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo anampatsa iye chipangano cha mdulidwe; ndipo kotero Abrahamu anabala Isaki, namdula tsiku lachisanu ndi chitatu; ndi Isaki anabala Yakobo, ndi Yakobo anabala makolo aakulu aja khumi ndi awiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo anampatsa iye chipangano cha mdulidwe; ndipo kotero Abrahamu anabala Isaki, namdula tsiku lachisanu ndi chitatu; ndi Isaki anabala Yakobo, ndi Yakobo anabala makolo akulu aja khumi ndi awiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Tsono Mulungu adachita chipangano ndi Abrahamu, chimene chizindikiro chake chinali kuumbala. Motero Abrahamu adaumbala mwana wake Isaki, ali ndi masiku asanu ndi atatu akubadwa. Isaki adaumbala Yakobe, ndipo Yakobe adaumbala makolo athu khumi ndi aŵiri aja.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Kenaka Mulungu anachita pangano la mdulidwe ndi Abrahamu. Ndipo Abrahamu, anabereka Isake, namudula ali ndi masiku asanu ndi atatu. Ndipo Isake anabereka Yakobo, Yakobo anabereka makolo khumi ndi awiri aja.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 7:8
20 Mawu Ofanana  

Pamene Yehova anaona kuti anamuda Leya, anatsegula m'mimba mwake; koma Rakele anali wouma.


Ndipo Biliha anatenga pakati, nambalira Yakobo mwana wamwamuna.


Ndipo anachokera ku Betele: ndipo panatsala nthawi asanafike ku Efurata: ndipo Rakele anabala navutidwa.


Ndipo pakutsirizika iye, pakuti anamwalira, anamutcha dzina lake Benoni; koma atate wake anamutcha Benjamini.


Ndipo Abrahamu anabala Isaki. Ana a Isaki: Esau, ndi Israele.


Abrahamu anabala Isaki; ndi Isaki anabala Yakobo; ndi Yakobo anabala Yuda ndi abale ake;


Chifukwa cha ichi Mose anakupatsani inu mdulidwe (si kuti uchokera kwa Mose, koma kwa makolo); ndipo mudula munthu tsiku la Sabata.


Amuna inu, abale, kuloleka kunena poyera posaopa kwa inu za kholo lija Davide, kuti adamwalira naikidwanso, ndipo manda ake ali ndi ife kufikira lero lino.


Tsono chinawerengedwa bwanji? M'mene iye anali wodulidwa kapena wosadulidwa? Si wodulidwa ai, koma wosadulidwa;


Abale, ndinena monga munthu. Pangano, lingakhale la munthu, litalunzika, palibe munthu aliyesa chabe, kapena kuonjezapo.


Ndipo ichi ndinena: Lamulo, limene linafika zitapita zaka mazana anai mphambu makumi atatu, silifafaniza pangano lolunzika kale ndi Mulungu, kuliyesa lonjezanolo lachabe.


Koma tapenyani ukulu wake wa iyeyu, amene Abrahamu, kholo lalikulu, anampatsa limodzi la magawo khumi la zosankhika za kunkhondo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa