Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 1:2 - Buku Lopatulika

2 Abrahamu anabala Isaki; ndi Isaki anabala Yakobo; ndi Yakobo anabala Yuda ndi abale ake;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Abrahamu anabala Isaki; ndi Isaki anabala Yakobo; ndi Yakobo anabala Yuda ndi abale ake;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Abrahamu adabereka Isaki, Isaki adabereka Yakobe, Yakobe adabereka Yuda ndi abale ake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Abrahamu anabereka Isake, Isake anabereka Yakobo, Yakobo anabereka Yuda ndi abale ake.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 1:2
27 Mawu Ofanana  

Mibadwo ya Isaki mwana wake wa Abrahamu ndi iyi: Abrahamu anabala Isaki:


Pambuyo pake ndipo anabadwa mphwake ndipo dzanja lake linagwira chitendeni cha Esau, ndi dzina lake linatchedwa Yakobo: ndipo Isaki anali wa zaka makumi asanu ndi limodzi pamene mkazi wake anabala iwo.


Ana a Abrahamu: Isaki, ndi Ismaele.


Ndipo Abrahamu anabala Isaki. Ana a Isaki: Esau, ndi Israele.


Koma iwe, Israele, mtumiki wanga, Yakobo, amene ndinakusankha, mbeu ya Abrahamu bwenzi langa;


Yang'anani kwa Abrahamu kholo lanu, ndi kwa Sara amene anakubalani inu; pakuti pamene iye anali mmodzi yekha ndinamuitana iye; ndipo ndinamdalitsa ndi kumchulukitsa.


A ana a Yuda, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;


Buku la kubadwa kwa Yesu Khristu, mwana wa Davide, mwana wa Abrahamu.


ndi Yuda anabala Perezi ndi Zera mwa Tamara; ndi Perezi anabala Hezironi; ndi Hezironi anabala Ramu;


Ndipo anampatsa iye chipangano cha mdulidwe; ndipo kotero Abrahamu anabala Isaki, namdula tsiku lachisanu ndi chitatu; ndi Isaki anabala Yakobo, ndi Yakobo anabala makolo aakulu aja khumi ndi awiri.


Ndi chikhulupiriro Sara yemwe analandira mphamvu yakukhala ndi pakati, patapita nthawi yake, popeza anamwerengera wokhulupirika Iye amene adalonjeza;


Pakuti kwadziwikadi kuti Ambuye wathu anatuluka mwa Yuda; za fuko ili Mose sanalankhule kanthu ka ansembe.


Mwa fuko la Yuda anasindikizidwa chizindikiro zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Rubeni zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Gadi zikwi khumi ndi ziwiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa