Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 21:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo Mulungu anati kwa Abrahamu, Usaipidwe nao, chifukwa cha mnyamatayo, ndi chifukwa cha mdzakazi wako; momwe monse akunenera iwe Sara umvere iwe mau ake; chifukwa kuti mwa Isaki zidzaitanidwa mbeu zako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo Mulungu anati kwa Abrahamu, Usaipidwe nao, chifukwa cha mnyamatayo, ndi chifukwa cha mdzakazi wako; momwe monse akunenera iwe Sara umvere iwe mau ake; chifukwa kuti mwa Isaki zidzaitanidwa mbeu zako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Koma Mulungu adauza Abrahamu kuti, “Mtima wako usavutike chifukwa cha mwanayo ndi mzikazi wako Hagara. Zonse zimene akukuuza Sara uchite, chifukwa Isakiyu ndi amene adzakhala kholo la zidzukulu zako monga momwe ndidakulonjezera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Koma Mulungu anamuwuza Abrahamu kuti, “Usamve chisoni motero ndi mnyamatayu ndi mdzakazi wakoyu. Mvetsera chilichonse chomwe Sara akukuwuza, chifukwa zidzukulu zako zidzachokera mwa Isake.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 21:12
8 Mawu Ofanana  

Ndipo Mulungu anati, Koma Sara mkazi wako adzakubalira iwe mwana wamwamuna; ndipo udzamutcha dzina lake Isaki; ndipo ndidzalimbikitsa naye pangano langa, kuti likhale pangano la nthawi zonse, la ku mbeu zake za pambuyo pake.


Koma pangano langa ndidzalimbikitsa ndi Isaki, amene Sara adzakubalira iwe nthawi yomwe ino chaka chamawa.


ndilalikira za chimaliziro kuyambira pachiyambi, ndi kuyambira nthawi zakale ndinena zinthu zimene zisanachitidwe; ndi kunena, Uphungu wanga udzakhala, ndipo ndidzachita zofuna zanga zonse;


Koma lembo linena chiyani? Taya kubwalo mdzakazi ndi mwana wake, pakuti sadzalowa nyumba mwana wa mdzakazi pamodzi ndi mwana wa mfulu.


amene kudanenedwa za iye, kuti, Mwa Isaki mbeu yako idzaitanidwa:


Ndipo Yehova ananena ndi Samuele, Umvere mau onse anthuwo alikulankhula nawe; popeza sindiwe anakukana, koma ndine anandikana, kuti ndisakhale mfumu yao.


Chifukwa chake tsono umvere mau ao; koma uwachenjeze kolimba, ndi kuwadziwitsa makhalidwe ake a mfumu imene idzawaweruza.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa