Ndipo Mulungu anati, Koma Sara mkazi wako adzakubalira iwe mwana wamwamuna; ndipo udzamutcha dzina lake Isaki; ndipo ndidzalimbikitsa naye pangano langa, kuti likhale pangano la nthawi zonse, la ku mbeu zake za pambuyo pake.
Genesis 21:10 - Buku Lopatulika Chifukwa chake anati kwa Abrahamu, Chotsa mdzakazi uyo, ndi mwana wake wamwamuna; chifukwa mwana wa mdzakazi uyo sadzalowa m'nyumba pamodzi naye mwana wanga Isaki. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake anati kwa Abrahamu, Chotsa mdzakazi uyo, ndi mwana wake wamwamuna; chifukwa mwana wa mdzakazi uyo sadzalowa m'nyumba pamodzi naye mwana wanga Isaki. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Sara ataona, adauza Abrahamu kuti, “Mchotseni mdzakaziyu pamodzi ndi mwana wake yemweyu. Mwana wa mdzakazi asadzalandireko chuma chanu chimene adzalandire mwana wanga Isaki.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndipo anati kwa Abrahamu, “Muchotse mdzakazi ndi mwana wake wamwamunayu, pakuti mwana wa kapolo sadzagawana chuma ndi mwana wanga Isake.” |
Ndipo Mulungu anati, Koma Sara mkazi wako adzakubalira iwe mwana wamwamuna; ndipo udzamutcha dzina lake Isaki; ndipo ndidzalimbikitsa naye pangano langa, kuti likhale pangano la nthawi zonse, la ku mbeu zake za pambuyo pake.
Koma pangano langa ndidzalimbikitsa ndi Isaki, amene Sara adzakubalira iwe nthawi yomwe ino chaka chamawa.
Ndipo Abrahamu anati, Chifukwa ndinati, Pompano palibe ndithu kumuopa Mulungu, ndipo adzandipha ine chifukwa cha mkazi wanga.
Koma kwa ana a akazi ake aang'ono amene Abrahamu anali nao Abrahamu anapatsa mphatso, nawachotsa iwo kwa Isaki mwana wake, akali ndi moyo, kuti anke kum'mawa, ku dziko la kum'mawa.
Pomwepo mfumu inati kwa atumiki, Mumange iye manja ndi miyendo, mumponye kumdima wakunja; komweko kudzali kulira ndi kukukuta mano.
Pakuti ngati kulowa nyumba kuchokera kulamulo, sikuchokeranso kulonjezano; koma kumeneku Mulungu anampatsa Abrahamu kwaufulu mwa lonjezano.
Kotero kuti sulinso kapolo, koma mwana; koma ngati mwana, wolowa nyumbanso mwa Mulungu.
kuti tilandire cholowa chosavunda ndi chosadetsa ndi chosafota, chosungikira mu Mwamba inu,
Anatuluka mwa ife, komatu sanali a ife; pakuti akadakhala a ife akadakhalabe ndi ife, koma kudatero kuti aonekere kuti sali onse a ife.
Ndipo mkazi wa Giliyadi anambalira ana aamuna; koma atakula ana aamuna a mkaziyo anampirikitsa Yefita, nanena naye, Sudzalandira cholowa m'nyumba ya atate wako; pakuti ndiwe mwana wa mkazi wina.