Oweruza 11:2 - Buku Lopatulika2 Ndipo mkazi wa Giliyadi anambalira ana aamuna; koma atakula ana aamuna a mkaziyo anampirikitsa Yefita, nanena naye, Sudzalandira cholowa m'nyumba ya atate wako; pakuti ndiwe mwana wa mkazi wina. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20142 Ndipo mkazi wa Giliyadi anambalira ana amuna; koma atakula ana amuna a mkaziyo anampirikitsa Yefita, nanena naye, Sudzalandira cholowa m'nyumba ya atate wako; pakuti ndiwe mwana wa mkazi wina. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa2 Giliyadi analinso ndi mkazi amene anali ndi ana. Tsono ana amenewo atakula, adampirikitsa Yefita namuuza kuti, “Sudzalandirako choloŵa m'nyumba ya bambo wathu, pakuti ndiwe mwana wa kwa mkazi wina.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero2 Mkazi wake wa Giliyadi anabereka naye ana aamuna. Tsono ana amenewa atakula anapirikitsa Yefita ndi kumuwuza kuti, “Sudzalandirako cholowa mʼnyumba ya abambo athu chifukwa ndiwe mwana wa mkazi wina.” Onani mutuwo |