Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Yohane 2:19 - Buku Lopatulika

19 Anatuluka mwa ife, komatu sanali a ife; pakuti akadakhala a ife akadakhalabe ndi ife, koma kudatero kuti aonekere kuti sali onse a ife.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Anatuluka mwa ife, komatu sanali a ife; pakuti akadakhala a ife akadakhalabe ndi ife, koma kudatero kuti aonekere kuti sali onse a ife.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Anthuwo adachita kuchoka pakati pathu, komabe sanali a gulu lathu kwenikweni. Pakuti akadakhala a gulu lathu, bwenzi akali nafebe. Koma adatichokera, kuti aonekere poyera kuti panalibe ndi mmodzi yemwe mwa iwo amene anali wa gulu lathu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Anthu amenewa anachoka pakati pathu, komatu sanali a mʼgulu lathu. Pakuti akanakhala a mʼgulu lathu, akanakhalabe nafe, koma kuchoka kwawo kunatisonyeza kuti sanali a mʼgulu lathu.

Onani mutuwo Koperani




1 Yohane 2:19
30 Mawu Ofanana  

Koma wolungama asungitsa njira yake, ndi iye wa manja oyera adzakulabe mumphamvu.


Pakuti Yehova akonda chiweruzo, ndipo sataya okondedwa ake. Asungika kosatha, koma adzadula mbumba za oipa.


Ngakhale bwenzi langa lenileni, amene ndamkhulupirira, ndiye amene adadyako mkate wanga, anandikwezera chidendene chake.


chifukwa Akhristu onama adzauka, ndi aneneri onama nadzaonetsa zizindikiro zazikulu ndi zozizwa: kotero kuti akanyenge, ngati nkotheka, osankhidwa omwe. Onani ndakuuziranitu pasadafike.


pakuti adzauka Akhristu onyenga ndi aneneri onyenga, ndipo adzachita zizindikiro ndi zozizwitsa, kuti akasocheretse, ngati nkutheka, osankhidwa omwe.


Ndipo za pathanthwe ndiwo amene, pakumva, alandira mau ndi kukondwera; koma alibe mizu; akhulupirira kanthawi, ndipo pa nthawi ya mayesedwe angopatuka.


Nthambi iliyonse ya mwa Ine yosabala chipatso, aichotsa; ndi iliyonse yakubala chipatso, aisadza, kuti ikabale chipatso chochuluka.


koma iye wakumwa madzi amene Ine ndidzampatsa sadzamva ludzu nthawi zonse; koma madzi amene Ine ndidzampatsa adzakhala mwa iye kasupe wa madzi otumphukira kumoyo wosatha.


Popeza tamva kuti ena amene anatuluka mwa ife anakuvutani ndi mau, nasocheretsa mitima yanu; amenewo sitinawalamulire;


ndipo mwa inu nokha adzauka anthu, olankhula zokhotakhota, kupatutsa ophunzira awatsate.


Koma sikuli ngati mau a Mulungu anakhala chabe ai. Pakuti onse akuchokera kwa Israele siali Israele;


Pakuti kuyenera kuti pakhale mipatuko mwa inu, kuti iwo ovomerezedwa aonetsedwe mwa inu.


Amuna ena opanda pake anatuluka pakati pa inu, nacheta okhala m'mzinda mwao, ndi kuti, Timuke titumikire milungu ina, imene simunaidziwe;


Mwa ichi ndipirira zonse, chifukwa cha osankhika, kuti iwonso akapeze chipulumutsocho cha mwa Khristu Yesu, pamodzi ndi ulemerero wosatha.


Koma ndithu maziko a Mulungu aimika pokhazikika, ndi kukhala nacho chizindikiro ichi, Ambuye azindikira iwo amene ali ake; ndipo, Adzipatule kwa chosalungama yense wakutchula dzina la Ambuye.


Koma sadzapitirirapo; pakuti kupusa kwao kudzaonekeratu kwa onse, monganso kupusa kwa iwo aja.


Koma ife si ndife a iwo akubwerera kulowa chitayiko; koma a iwo a chikhulupiriro cha ku chipulumutso cha moyo.


Pakuti onyenga ambiri adatuluka kulowa m'dziko lapansi, ndiwo amene savomereza kuti Yesu Khristu anadza m'thupi. Ameneyo ndiye wonyenga ndi wokana Khristu.


Yuda, kapolo wa Yesu Khristu, ndi mbale wa Yakobo, kwa iwo oitanidwa, okondedwa mwa Mulungu Atate, ndi osungidwa ndi Yesu Khristu:


Iwo ndiwo opatukitsa, anthu a makhalidwe achibadwidwe, osakhala naye Mzimu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa