Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 25:6 - Buku Lopatulika

6 Koma kwa ana a akazi ake aang'ono amene Abrahamu anali nao Abrahamu anapatsa mphatso, nawachotsa iwo kwa Isaki mwana wake, akali ndi moyo, kuti anke kum'mawa, ku dziko la kum'mawa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Koma kwa ana a akazi ake ang'ono amene Abrahamu anali nao Abrahamu anapatsa mphatso, nawachotsa iwo kwa Isaki mwana wake, akali ndi moyo, kuti anke kum'mawa, ku dziko la kum'mawa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Koma asanafe adaŵapatsako mphatso ana ake ena aja amene adaŵabereka mwa akazi ake enawo. Onsewo adaŵatumiza ku dziko lakuvuma kuti akakhale kumeneko, kuŵachotsa kwa mwana wake Isaki.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Koma pamene anali ndi moyo, Abrahamu anapereka mphatso kwa ana aakazi ake ena onse. Kenaka anawatumiza ku dziko la kummawa kuti akhale kutali ndi mwana wake Isake.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 25:6
18 Mawu Ofanana  

Ndipo Sarai mkazi wake wa Abramu anatenga Hagara mdzakazi wake wa ku Ejipito, Abramu atakhala m'dziko la Kanani zaka khumi, nampereka iye kwa Abramu mwamuna wake, kuti akhale mkazi wake.


Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa, natenga mkate ndi thumba la madzi, nampatsa Hagara, naika paphewa pake, ndi mwana, namchotsa iye: ndipo iye anamuka, nasocherera m'chipululu cha Beereseba.


Ndipo Abrahamu anatenga mkazi wina dzina lake Ketura.


Ndipo Yakobo ananka ulendo wake, nafika ku dziko la anthu a kum'mawa.


Ndipo Rakele anampatsa iye Biliha mdzakazi wake akhale mkazi wake; ndipo Yakobo analowa kwa iye.


Pamene Leya anaona kuti analeka kubala, anatenga Zilipa mdzakazi wake, nampatsa iye kwa Yakobo kuti akhale mkazi wake.


Ndipo anauka usiku womwewo, natenga akazi ake awiri, ndi adzakazi ake awiri, ndi ana ake aamuna khumi ndi mmodzi, naoloka pa dooko la Yaboki.


Ndipo panali pamene Israele anakhala m'dzikomo, Rubeni anamuka nagona ndi Biliha, mkazi wamng'ono wa atate wake: ndipo Israele anamva. Ana aamuna a Yakobo anali khumi ndi awiri:


Ndipo Rehobowamu anakonda Maaka mwana wamkazi wa Abisalomu koposa akazi ake onse, ndi akazi ake aang'ono (pakuti adatenga akazi khumi mphambu asanu ndi atatu, ndi akazi aang'ono makumi asanu ndi limodzi, nabala ana aamuna makumi awiri mphambu asanu ndi atatu, ndi ana aakazi makumi asanu ndi limodzi).


Panali munthu m'dziko la Uzi, dzina lake ndiye Yobu; ndipo munthuyu anali wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu ndi kupewa zoipa.


Zoweta zakenso zinali nkhosa zikwi zisanu ndi ziwiri, ndi ngamira zikwi zitatu, ndi ng'ombe zamagoli mazana asanu, ndi abulu aakazi mazana asanu, antchito ake omwe ndi ambiri; chotero munthuyu anaposa anthu onse a kum'mawa.


kotero kuti mukakhale ana a Atate wanu wa Kumwamba; chifukwa Iye amakwezera dzuwa lake pa oipa ndi pa abwino, namavumbitsira mvula pa olungama ndi pa osalungama.


Koma sanadzisiyire Iye mwini wopanda umboni, popeza anachita zabwino, nakupatsani inu zochokera kumwamba mvula ndi nyengo za zipatso, ndi kudzaza mitima yanu ndi chakudya ndi chikondwero.


Ndipo mpongozi wake, ndiye atate wa mkaziyo, anamuimika kuti akhale naye masiku atatu; nadya namwa nagona komweko.


Ndipo kunali, akabzala Israele, amakwera Amidiyani, ndi Amaleke, ndi ana a kum'mawa, inde amawakwerera;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa