Ndipo Mulungu analitcha thambolo Kumwamba. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachiwiri.
Genesis 1:9 - Buku Lopatulika Ndipo anati Mulungu, Madzi a pansi pakumwamba asonkhane pamodzi pamalo amodzi, uoneke mtunda: ndipo kunatero. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anati Mulungu, Madzi a pansi pa kumwamba asonkhane pamodzi pa malo amodzi, uoneke mtunda: ndipo kunatero. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mulungu adatinso, “Madzi apansiŵa akhale pa malo amodzi, kuti paoneke mtunda,” ndipo zidachitikadi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mulungu anati, “Madzi a pansi pa thambo asonkhane pa malo amodzi kuti mtunda uwoneke,” ndipo zinachitikadi. |
Ndipo Mulungu analitcha thambolo Kumwamba. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachiwiri.
Inu ndinu Yehova, nokhanu; mwalenga thambo, kumwambamwamba, ndi khamu lao lonse, dziko lapansi, ndi zonse zili pomwepo, nyanja ndi zonse zili m'mwemo, ndi Inu muzisunga zamoyo zonsezi, ndi khamu lakumwamba lilambira Inu.
Amene alumikiza mitanda ya zipinda zake m'madzi; naika makongwa akhale agaleta ake; nayenda pa mapiko a mphepo.
Mitsinje yonse ithira m'nyanja, koma nyanja yosadzala; komwe imukira mitsinjeyo, komweko ibweranso.
Kodi simundiopa Ine? Ati Yehova: simudzanthunthumira pamaso pa Ine, amene ndinaika mchenga chilekaniro cha nyanja, ndi lemba lamuyaya kuti isapitirirepo? Ndipo ngakhale mafunde ake achita gavigavi, alephera; ngakhale akokoma, sangathe kupitirirapo.
Ndipo ananena nao, Ndine Muhebri, ndiopa Yehova Mulungu wa Kumwamba, amene analenga nyanja ndi mtunda.
Pakuti ichi aiwala dala, kuti miyamba inakhala kale lomwe, ndi dziko lidaungika ndi madzi ndi mwa madzi, pa mau a Mulungu;
nalumbira kutchula Iye amene ali ndi moyo kunthawi za nthawi, amene analenga m'mwamba ndi zinthu zili momwemo, ndi dziko lapansi ndi zinthu zili momwemo, ndi nyanja ndi zinthu zili momwemo kuti sipadzakhalanso nthawi: